January 7-13
MACHITIDWE 21-22
Nyimbo 55 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Cifunilo ca Yehova Cicitike”: (10 min.)
Mac. 21:8-12—Akhristu anzake anamucondelela Paulo kuti asapite ku Yerusalemu, cifukwa ca zoopsa zimene zinali kudzamucitikila (bt mape. 177-178 mapa. 15-16)
Mac. 21:13—Paulo anatsimikiza mtima kucita cifunilo ca Yehova (bt peji 178 pala. 17)
Mac. 21:14—Abalewo ataona kuti Paulo walimbikila kupita, anamuleka (bt peji 178 pala. 18)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Mac. 21:23, 24—Popeza kuti Akhristu sanali pansi pa Cilamulo ca Mose, n’cifukwa ciani akulu a ku Yerusalemu anapatsa Paulo malangizo aya? (bt mape. 184-185 mapa. 10-12)
Mac. 22:16—Kodi macimo a Paulo anasambitsidwa bwanji? (“kusamba kuti ucotse macimo ako mwa kuitana pa dzina lake” nwtsty mfundo younikila)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Mac. 21:1-19 (th phunzilo 5)a
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa: (10 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Mawu Oyamba Ogwila Mtima, ndiyeno kambilanani phunzilo 1 m’kabulosha ka Kuphunzitsa.
Nkhani: (5 min. olo kucepelapo) w10 2/1 peji 13 pala. 2 mpaka peji 14 pala. 2—Mutu: Kodi Akhristu Ayenela Kusunga Sabata ya Wiki Iliyonse? (th phunzilo 1)b
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Yehova Anatiphunzitsa Kulela Bwino Ana Athu”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 49
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 70 na Pemphelo