UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Mudzacita Ciani pa Nthawi ya Cilala?
Cikhulupililo na cidalilo zimayendela limodzi. Mwacitsanzo, kukhulupilila kwambili Yehova kumatithandiza kukhala na cidalilo cakuti adzatiteteza na kutisamalila. (Sal. 23:1, 4; 78:22) Pamene mapeto a dongosolo lino la zinthu akutiyandikila, Satana adzatiukila koopsa. (Chiv. 12:12) N’ciani cidzatithandiza pa nthawiyo?
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI KODI MUDZACITA CIANI PA NTHAWI YA CILALA? PAMBUYO PAKE, KAMBILANANI MAFUNSO AYA:
Kodi tingafanane bwanji na “mtengo” wochulidwa pa Yeremiya 17:8?
Chulankoni vuto limodzi limene lili ngati “kutentha.”
Kodi “mtengo” uja unakhudzidwa bwanji? Nanga n’cifukwa ciani?
Kodi Satana amafuna kuwononga ciani?
Kodi tili ngati anthu ojaila kuyenda pa ndeke m’njila yanji?
N’cifukwa ciani tifunika kupitiliza kukhulupilila kapolo wokhulupilika ndi wanzelu? Nanga kodi kukhulupilika kwathu kungayesedwe bwanji?
N’cifukwa ciani tifunika kupitiliza kukhulupilila mfundo za m’Baibo olo kuti ena atiseke?