September 23-29
AHEBERI 12-13
Nyimbo 88 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Cilango—Umboni Wakuti Yehova Amatikonda”: (10 min.)
Aheb. 12:5—Musataye mtima mukapatsidwa cilango (w12 3/15 29 ¶18)
Aheb. 12:6, 7—Yehova amalanga anthu amene amawakonda (w12 7/1 21 ¶3)
Aheb. 12:11—Ngakhale kuti nthawi zina cilango cimaŵaŵa pocilandila, cimatithandiza kukhala atumiki abwino a Mulungu (w18.03 32 ¶18)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Aheb. 12:1—Kodi citsanzo ca “mtambo wa mboni waukulu” cimatilimbikitsa bwanji? (w11 9/15 17-18 ¶11)
Aheb. 13:9—Kodi vesiyi itanthauza ciani? (w89 12/15 22 ¶10)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Aheb. 12:1-17 (th phunzilo 11)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 2)
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) lvs 39-40 ¶19 (th phunzilo 6)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Pililani Olo kuti . . . Muli na Zofooka: (5 min.) Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno kambilanani mafunso otsatilawa:
Kodi M’bale Cázares anali kulimbana na vuto lanji kucokela pamene anabatizika?
Kodi m’baleyu anapatsidwa cilango m’njila ziti?
Zofunikila za Mpingo: (10 min.)
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 85
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 74 na Pemphelo