CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 12-13
Cilango—Umboni Wakuti Yehova Amatikonda
12:5-7, 11
Cilango cimatanthauza kukwapula, kuwongolela, kulangiza, na kuphunzitsa. Monga mmene tate wacikondi amalangila ana ake, Yehova naye amatilanga. Timalandila cilango cake mwa njila izi . . .
Kuŵelenga Baibo, kucita phunzilo laumwini, kupezeka pa misonkhano, na kusinkha-sinkha
Wokhulupilila mnzathu akatipatsa uphungu kapena kutiwongolela
Zotulukapo za kulakwa kwathu
Kudzudzulidwa kapena kucotsedwa mu mpingo
Kukumana na mayeselo kapena cizunzo cimene Yehova walola.—w15 9/15 21 ¶13; it-1 629