UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khalani Wodzicepetsa—Pewani Kudzitamandila
Kudzitamandila kumaonetsa kuti munthu ni wonyada, ndiponso sikuthandiza amene akutimvetsela. N’cifukwa cake, Baibo imati: “Mlendo akutamande, osati pakamwa pako.”—Miy. 27:2.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI KHALA BWENZI LA YEHOVA—KHALA WODZICEPETSA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Ni zinthu ziti zofala zimene anthu amakonda kudzitamandilapo?
Kodi Kalebe anali kudzitamandila za ciani kwa mnzake?
Kodi atate ake a Kalebe anam’thandiza bwanji kumvetsa mfundo ya kufunika kokhala wodzicepetsa?
Kodi mfundo ya pa 1 Petulo 5:5, ingatithandize bwanji kukhala wodzicepetsa?