CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Zimene Tingacite Kuti Tilandile Madalitso a Yehova
Pewani kulambila milungu yopanda pake (Lev. 26:1; w08 4/15 4 ¶8)
Lambilani Yehova mmene iye amafunila (Lev. 26:2; it-1 223 ¶3)
Muzimvela malamulo ake (Lev. 26:3, 12; w91 3/1 17 ¶10)
Aisiraeli amene anali kuyesetsa kutsatila malamulo a Yehova anali kukhala pa ubwenzi wabwino na iye, komanso anali kulandila madalitso ambili.
Pa zinthu zotsatilazi, ni ziti zimene imwe muli nazo kaamba ka dalitso la Yehova?
Cidziŵitso colondola ca m’Baibo
Mtendele wa maganizo
Banja lacimwemwe
Ciyembekezo ca tsogolo labwino