LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 July tsa. 5
  • Katumikilen’koni ku Malo Osoŵa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Katumikilen’koni ku Malo Osoŵa
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi ku Ofesi ya Nthambi Kumacitika Nchito Yanji?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Njila Zowonjezela Utumiki Wanu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Oyang’anila Oweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • “Ine Ndilipo! Nditumizeni.”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 July tsa. 5
Zithunzi za mu vidiyo yakuti “Loŵani pa Khomo la Zocita Zambili M’cikhulupililo—Katumikilenkoni ku Malo Osowa.” Zithunzi: 1. Gabriel akufufuza. 2. Akukambilana na mkulu za mmene angalembele kalata yopita ku ofesi ya nthambi. 3. Akulalikila na mnzake Samuel pa nthawi ya kampeni yapadela ya ulaliki.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU | DZIIKILENI ZOLINGA ZA CAKA CA UTUMIKI CATSOPANO

Katumikilen’koni Kumalo Osoŵa

Pamafunika cikhulupililo kuti munthu acoke m’dela limene anazoloŵela, na kusamukila ku dela lina pofuna kuwonjezela zocita mu utumiki wake. (Aheb. 11:8-10) Ngati muli na colinga cokatumikila ku dela losoŵa, kambilanani na akulu a mumpingo wanu. Kodi mungacite ciyani kuti mudziŵe ngati mungakwanitse kusamukila kosoŵa? Nanga mungasankhe bwanji malo oyenela kusamukilako? Ŵelengani zimene zinafalitsidwa mu zofalitsa zathu pa nkhani yosamukila kosoŵa. Kambilanani na ofalitsa amene anakatumikilako ku mpingo wosoŵa. (Miy. 15:22) Pemphani citsogozo ca Yehova kupitila m’pemphelo. (Yak. 1:5) Dziŵani zambili za malo amene muganizila zokatumikilako. Ndipo ngati n’kotheka, pitani kukaona malowo kukali nthawi musanapange cisankho.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI LOŴANI PA KHOMO LA ZOCITA ZAMBILI M’CIKHULUPILILO —KATUMIKILEN’KONI KUMALO OSOŴA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi ni zopinga zotani zimene Gabriel anakumana nazo, nanga n’ciyani cinamuthandiza kuzigonjetsa?

Ngati mufuna kudziŵa zambili za mipingo yapafupi imene ni yosoŵa, kambilanani na woyang’anila dela wanu. Koma ngati mufuna kudziŵa zambili za mipingo yakutali imene ni yosoŵa, lembelani kalata ofesi yanu ya nthambi kupitila m’Komiti ya Utumiki ya Mpingo wanu. Ngati mipingoyo ili m’gawo loyang’anilidwa na nthambi ina, lembelani kalata nthambi imene imayang’anila kumeneko. Ngati pali malo ena ake amene mungakonde kupitako, achuleni m’kalatayo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani