Dziŵani Zoona Zeni-Zeni
Cifukwa Cake Zingakhale Zovuta
Tsankho limayamba cifukwa cakuti munthu anamvela kapena kuuzidwa mfundo zabodza. Ganizilani zitsanzo izi:
Mabwana ena amakhulupilila kuti akazi sangakwanitse kugwila nchito zofuna luso lapadela, mphamvu zambili kapena kuganiza kwambili.
M’nthawi ya Europe wamakedzana, Ayuda anali kuwanamizila kuti anali kuthila poizoni m’zitsime na kuyambukiza anthu matenda. Mu ulamulilo wa Nazi, Ayuda anawanamizilanso. Koma panthawiyi anawanamizila kuti ndiwo anapangitsa mavuto azacuma m’dziko la Germany. Zocitika zonsezi zinapangitsa kuti Ayuda azisalidwa kwambili, ndipo zimenezi zimaonekela mpaka pano.
Anthu ambili amaganiza kuti munthu aliyense wolemala amakhala wosasangalala kapena wamkali.
Anthu amene amakhulupilila nkhambakamwa ngati zimenezi, angapeleke zitsanzo kapena mfundo zina zosadalilika zimene amati ni umboni wotsimikizila kuti maganizo awo ni olondola. Ndipo amaona kuti aliyense amene sagwilizana na maganizo awo ni wosadziŵa zinthu.
Mfundo ya m’Baibo
“Si bwino kuti munthu akhale wosadziwa zinthu.”—MIYAMBO 19:2.
Kodi Mfundo Imeneyi Itanthauza Ciani? Munthu amene sadziŵa zoona zeni-zeni, amapanga zosankha zolakwika. Ngati tikhulupilila mfundo zopanda umboni, tingayambe kuwaganizila molakwika anthu ena.
Kodi Kudziŵa Zoona Zeni-zeni Kumathandiza Bwanji?
Ngati tidziŵa zoona zeni-zeni ponena za anthu enaake, sitingathamangile kukhulupilila mabodza amene ena amakamba ponena za iwo. Ndipo tikadziŵa kuti zimene tinamva zokhudza gulu linalake la anthu n’zabodza, tingasinthe maganizo athu n’kuyamba kuwaona moyenela anthuwo.
Zimene Mungacite
Olo ena akambe kuti anthu a mtundu wakuti-wakuti ali na khalidwe linalake loipa, kumbukilani kuti si anthu onse a mtunduwo ali na khalidwe limenelo.
Kumbukilani kuti pangakhale zambili zimene simudziŵa ponena za anthu ena.
Fufuzani ku magwelo odalilika kuti mudziŵe zoona zeni-zeni.