LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g20 na. 3 masa. 12-13
  • Onetsani Cikondi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Onetsani Cikondi
  • Galamuka!—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Cifukwa Cake Zingakhale Zovuta
  • Mfundo ya m’Baibo
  • Zimene Mungacite
  • Anagonjetsa Tsankho
    Galamuka!—2020
  • Tsankho—Kodi Na Imwe Muli Nalo?
    Galamuka!—2020
  • Tikhale Amodzi, Monga Mmene Yehova na Yesu Alili Amodzi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Dziŵani Zoona Zeni-zeni
    Galamuka!—2020
Onaninso Zina
Galamuka!—2020
g20 na. 3 masa. 12-13
Mayi wa cimwenye akuthandiza mayi wokalamba wa ci Caucasian kukwela masitepe, ndipo ku dzanja linalo wanyamula zakudya za mayiyo.

Onetsani Cikondi

Cifukwa Cake Zingakhale Zovuta

Tsankho limatenga nthawi kuti lithe. Mofanana na kalombo koyambitsa matenda, kamene kamafuna khama na nthawi kuti tikagonjetse, tsankho nalonso limafuna nthawi na khama kuti tilithetse. Kodi mungacite ciani kuti mucotse tsankho mumtima mwanu?

Mfundo ya m’Baibo

Zithunzi: 1. Munthu wa ci Asian wagwila citseko kuti munthu wa cikuda amene wanyamula makapu a khofi adutse. 2. Munthu wa cikuda mmodzi-modziyo akupatsa khofi anzake amene amaseŵenza nawo, kuphatikizapo mayi uja wa cimwenye amene tamuchulapo kale.

“Valani cikondi, pakuti cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.” —AKOLOSE 3:14.

Kodi mfundo imeneyi itanthauza ciani? Kucitila ena zinthu zabwino kumathandiza kuti muyambe kugwilizana nawo. Ndipo ngati muyesetsa kuonetsa cikondi kwa anthu, tsankho limacepela-cepela mumtima mwanu. Cikondi cikamakula mumtima mwanu, nawonso maganizo oipidwa na ŵanthu ŵena amacepa.

Zimene Mungacite

Zithunzi: 1. Mayi wokalamba wa ci Caucasian akukwela masitepe mothandizidwa na mayi wa cimwenye amenenso wanyamula zakudya za mayiyo. 2. Mayi wokalamba mmodzi-modziyo akupatsa zakudya mnansi wake amene ni munthu uja wa ci Asian tamuchulapo kale.

Ganizilani zimene mungacite poonetsa cikondi kwa anthu amene mumawaganizila kuti sali bwino. Zinthu zake sizicita kufunikila kukhala zapamwamba. Yesani kucita zinthu monga izi:

Cinthu ciliconse cabwino cimene mwacitila munthu, cimakuthandizani kucepetsa tsankho mumtima mwanu

  • Onetsani ulemu kwa anthu amenewo mwa kuwagwilila citseko kuti aloŵe kapena kupatsa mmodzi wa iwo malo anu okhala pamene muli pa ulendo.

  • Yesani kucezako nawo mwacidule, olo kuti mwina sadziŵa kukamba bwino citundu canu.

  • Khalani oleza mtima ngati acita zinthu m’njila imene muona kuti ni yacilendo.

  • Pamene afotokoza mavuto awo, onetsani kuti muwamvelela cifundo.

Citsanzo ca Zocitika Zeni-Zeni: Nazaré wa ku (Guinea-Bissau)

“Pa nthawi ina, n’nali kuona kuti anthu ocokela ku maiko ena si abwino, cifukwa n’nauzidwa kuti ambili mwa iwo amanama ku boma n’colinga cakuti liwapatse ndalama kapena thandizo lina. N’namvelanso kuti amakonda kucita zinthu zophwanya malamulo. Izi zinacititsa kuti niziwakayikila. Komabe, sin’nali kudziona ngati watsankho, cifukwa umu ni mmene ambili m’dela lathu anali kuonela anthu ocokela ku maiko ena.

“Koma m’kupita kwa nthawi, n’nazindikila kuti n’nali na tsankho. Koma malangizo anzelu a m’Baibo anithandiza kuti niyambe kucita zinthu mwacikondi na ŵanthu ocokela ku maiko ena. Tsopano siniwapewa. Koma nimawapatsa moni na kukamba nawo. Nimayesetsa kudziŵa bwino aliyense wa iwo. Lomba nimawaona moyenela, ndipo nimamasuka nawo kwambili.”

“N’nali Kufuna Kugwebana na Kupanda Cilungamo”

Rafika Morris.

Rafika analoŵa m’gulu la anthu ofuna kugwebana na khalidwe la kusankhana mitundu. Koma pamene anapezeka pa msonkhano wacigawo wa Mboni za Yehova, anapeza mgwilizano umene anali kufuna.

Tambani vidiyo yakuti Rafika Morris: N’nali Kufuna Kugwebana na Kupanda Cilungamo. Isakileni vidiyo imeneyi pa jw.org mwa kulemba mutu umenewu pa batani lofufuzila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani