LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g20 na. 3 masa. 10-11
  • Pezani Mabwenzi a Mitundu Yosiyana-siyana

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pezani Mabwenzi a Mitundu Yosiyana-siyana
  • Galamuka!—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Cifukwa Cake Zingakhale Zovuta
  • Mfundo ya m’Baibo
  • Kodi kupeza mabwenzi a mitundu yosiyana-siyana kumathandiza bwanji?
  • Zimene Mungacite
  • Anagonjetsa Tsankho
    Galamuka!—2020
  • Onetsani Cikondi
    Galamuka!—2020
  • Sankhani Anzanu Mwanzelu
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Maphunzilo Aumulungu Amagonjetsa Tsankho
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
Onaninso Zina
Galamuka!—2020
g20 na. 3 masa. 10-11
Azimayi anayi a mitundu yosiyana-siyana akuceza na kuseka pamene ana awo akuseŵela pa malo ocitilapo maseŵela.

Pezani Mabwenzi A Mitundu Yosiyana-siyana

Cifukwa Cake Zingakhale Zovuta

Ngati timapewa kupanga ubwenzi na ŵanthu amene timawaona ngati si abwino, tsankho lathu limakulila-kulila. Ndipo ngati tili na mabwenzi okha-okha amene amafanana na ife, tingayambe kuganiza kuti ife cabe ndiye timaganiza na kucita zinthu m’njila yoyenela.

Mfundo ya m’Baibo

“Futukulani mtima wanu.” —2 AKORINTO 6:13.

Kodi mfundo imeneyi itanthauza ciani? “Mtima” wathu ungatanthauze cikondi cimene tili naco. Ngati timakonda anthu okhawo amene amafanana na ife, cikondi cathu cimacepa. Kuti tipewe vuto limeneli, tifunika kukhala okonzeka kupanga ubwenzi na ŵanthu amene ni osiyana na ife.

Kodi kupeza mabwenzi a mitundu yosiyana-siyana kumathandiza bwanji?

Anthu tikawadziŵa bwino, timayamba kumvetsa cifukwa cake amacita zinthu mosiyana na mmene ife timacitila. Ndipo tikayamba kuwakonda, timaona kuti iwo na ife ndife amodzi. Timayamba kuwakonda kwambili na kuwamvelela cifundo.

Ganizilani citsanzo ca Nazaré. Poyamba iye anali kuona kuti anthu ocokela ku maiko ena si abwino. Iye anafotokoza cimene cinam’thandiza. Anati: “N’nali kuceza nawo na kuseŵenza nawo. N’nakumana na ŵanthu amene ena anali kuwanenela zoipa. Koma zimene n’napeza zinali zosiyana kwambili na zimene n’namvela. Ukapanga ubwenzi na ŵanthu acikhalidwe cina, umathetsa maganizo a tsankho amene unali nawo pa iwo, ndipo umayamba kuwakonda na kuona aliyense wa iwo kukhala wofunika.”

Samalani Posankha Mabwenzi

Anthu ena ali na makhalidwe oipa. Amacita zinthu zimene zingawavulaze na kuvulazanso ena. Conco, tifunika kusamala posankha mabwenzi. Si tsankho kupewa anthu acinyengo amene amacita makhalidwe oipa. Sikuti tifunika kucita zinthu zimene zingavulaze anthu amene amaphwanya mfundo za makhalidwe abwino kapena kuwalanda ufulu wawo ayi. Ngakhale n’telo, ni cinthu canzelu kusapalana nawo ubwenzi anthu aconco.—Miyambo 13:20.

Zimene Mungacite

Sakilani mipata yokamba na ŵanthu ocokela ku maiko ena, a mtundu wina, kapena okamba citundu cosiyana na canu. Mungacite izi:

  • Mungawapemphe kuti akuuzenkoni zina zokhudza umoyo wawo.

  • Mungawapemphe kuti akadye namwe cakudya.

  • Mvetselani mwachelu pamene akamba zokhudza umoyo wawo. Yesetsani kudziŵa zimene amaona kuti n’zofunika kwambili pa umoyo wawo.

Mukadziŵa zimene iwo akumana nazo pa umoyo na mmene zakhudzila khalidwe lawo, mungayambe kuwaona moyenela anthu amenewo komanso ena a mtundu wawo.

Citsanzo ca Zocitika Zeni-Zeni: Kandasamy na Sookammah a ku (Canada)

“Tinakulila m’dziko la South Africa panthawi ya tsankho loopsa. Anthu a mitundu yosiyana-siyana anali kukakamizidwa kukhala m’madela osiyana. Zimenezi zinawonjezela vuto la kusankhana mitundu. Ife sindife azungu, ndipo tinali kuwazonda maningi azungu cifukwa ena mwa iwo anali kutiona ngati otsika. Panthawiyo, sitinali kudziona ngati a tsankho. Koma tinali kuona kuti ifeyo ndi amene tikucitilidwa tsankho.

“Kuti tisinthe maganizo athu, tinayesetsa kufutukula mtima wathu na kupanga ubwenzi na ŵanthu a mitundu yosiyana-siyana. Pamene tinayamba kuceza na azungu, tinazindikila kuti tinali ofanana m’zambili. Tonse timakumana na zinthu zofanana mu umoyo. Timakumananso na mavuto ofanana.

“Tinafika ngakhale pocelezako mzungu wina na mkazi wake pa nyumba pathu kwa nthawi yaitali. Tinawadziŵa bwino. Posapita nthawi, tinayamba kuonana kuti ndife mabwenzi komanso kuti ndife ofanana. Zotulukapo zake n’zakuti azungu onse tinayamba kuwaona moyenela.”

Abale eni-eni

Johny na Gideon akupatsa moni ana kunja kwa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.

Johny na Gideon anakhala mabwenzi apamtima olo kuti anali a mitundu yosiyana ndiponso anali na maganizo osiyana pandale.

Tambani vidiyo yakuti Johny na Gideon: Anali Adani, Tsopano ni Abale. Isakileni vidiyo imeneyi pa jw.org mwa kulemba mutu umenewu pa batani lofufuzila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani