Nyimbo 152
Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu
Yopulinta
Daunilodi
(Miyambo 14:26)
O Yehova, munalonjeza
za moyo wosatha.
Tifuna kuuza ena
za lonjezo lanu.
Mavuto amatifoketsa,
Tisoŵa na cocita.
Komanso timaiŵala
za lonjezo lanu.
(KOLASI)
Ise timakudalilani
M’lungu
kuti mudzatithandiza.
Pamene tikulalikila anthu
tipeza mphamvu
mwa imwe.
Tithandizeni kukumbuka
kuti mumatikonda.
Ngakhale timavutika,
Simumatisiya.
Tilalikila mosaopa
kwa amene tapeza.
Mumatilimbitsa mtima
Pophunzitsa anthu.
(KOLASI)
Ise timakudalilani
M’lungu
kuti mudzatithandiza.
Pamene tikulalikila anthu
tipeza mphamvu
mwa imwe.
(Onaninso Sal. 72:13,14; Miy. 3:5, 6, 26; Yer. 17:7.)