NYIMBO 69
Patsogolo na Ulaliki wa Ufumu!
Yopulinta
	(2 Timoteyo 4:5)
- 1. Pitani, kalalikileni - Kwa amitundu yonse. - Na mtima wokonda anansi, - Thandizani ofatsa. - Ni mwayi wathu kulengeza - Za Ufumu wa Yehova. - Mokondwa tiphunzitsa ena, - Za dzina lake loyela. - (KOLASI) - Lalikani uthenga wa Ufumu - konse konse. - Khalanibe okhulupilika - kwa M’lungu wathu. 
- 2. Capamodzi titumikile - Yehova, ‘tate wathu. - Odzozedwa na nkhosa zina, - Tiphunzitse co’nadi. - Onse tiŵauze uthenga, - Wa Ufumu wa Yehova. - Tilengeza molimba mtima - Timadalila Yehova. - (KOLASI) - Lalikani uthenga wa Ufumu - konse konse. - Khalanibe okhulupilika - kwa M’lungu wathu. 
(Onaninso Sal. 23:4; Mac. 4:29, 31; 1 Pet. 2:21.)