NYIMBO 91
Nchito Yoonetsa Cikondi Cathu
Yopulinta
(Salimo 127:1)
1. Tifuna kupemphela;
Kuti ‘se tiyamikile.
Inu Yehova pa cikondi,
Mwationetsa!
Imwe mwatidalitsa,
Pogwila nchito mwakhama.
Takumangilani nyumbayi,
Na manja athu.
(KOLASI)
Unali mwayi wapadela
Kukumangilani nyumba.
Tidzakutamandani M’lungu nthawi zonse
Na kukutumikilani.
2. Ndife osangalala,
Kuti tapeza mabwenzi!
Tidzakumbukila nthawizi
Ku umuyaya!
Taona mzimu wanu,
Pogwila nchito pamodzi.
Dzina lanu talichukitsa;
Kwa anthu onse!
(KOLASI)
Unali mwayi wapadela
Kukumangilani nyumba.
Tidzakutamandani M’lungu nthawi zonse
Na kukutumikilani.
(Onaninso Sal. 116:1; 147:1; Aroma 15:6.)