NYIMBO 110
“Cimwemwe Cimene Yehova Amapeleka”
Yopulinta
(Nehemiya 8:10)
1. Ufumu wa Yehova wayandika,
Tilalikile kwa onse.
Kwezani maso ndipo kondwelani,
Cipulumutso cafika!
(KOLASI)
Tiyeni titamande Yehova,
Amatipatsa cimwemwe.
Mokondwa tiyeni tiyamikile,
Watipatsa ciyembekezo.
Tiyeni titamande Yehova.
Anthu onse amudziŵe.
Modzipeleka timutumikile,
Ndipo tidzapeza cimwemwe.
2. Dalilani Yehova musayope.
Cifukwa iye ngwamphamvu.
Nyamukani, imbani mofuula;
Imbani mosangalala.
(KOLASI)
Tiyeni titamande Yehova,
Amatipatsa cimwemwe.
Mokondwa tiyeni tiyamikile,
Watipatsa ciyembekezo.
Tiyeni titamande Yehova.
Anthu onse amudziŵe.
Modzipeleka timutumikile,
Ndipo tidzapeza cimwemwe.
(Onaninso 1 Mbiri 16:27; Sal. 112:4; Luka 21:28; Yoh. 8:32.)