Tsiku Lacitatu
“Limba mtima ndipo ucite zinthu mwamphamvu. Yembekezela Yehova” —SALIMO 27:14
KUM’MAŴA
8:20 Vidiyo ya Nyimbo
8:30 Nyimbo Na. 73 na Pemphelo
8:40 YOSIILANA: Zocitika Zam’tsogolo Zimene Zidzafuna Kulimba Mtima
Kulengeza “Bata ndi Mtendele!” (1 Atesalonika 5:2, 3)
Kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu (Chivumbulutso 17:16, 17)
Kulengeza Uthenga wa Matalala (Chivumbulutso 16:21)
Kuukila kwa Gogi wa Magogi (Ezekieli 38:10-12, 14-16)
Aramagedo (Chivumbulutso 16:14, 16)
Nchito Yaikulu Yokonzanso Zinthu (Yesaya 65:21)
Ciyeso Cotsiliza (Chivumbulutso 20:3, 7, 8)
10:10 Nyimbo Na. 8 na Zilengezo
10:20 NKHANI YA ANTHU ONSE: Kodi Ciyembekezo ca Ciukililo Cimatithandiza Bwanji Kukhala Olimba Mtima? (Maliko 5:35-42; Luka 12:4, 5; Yohane 5:28, 29; 11:11-14)
10:50 Cidule ca Nsanja ya Mlonda
11:20 Nyimbo Na. 151 na Kupumula
KUMASANA
12:35 Vidiyo ya Nyimbo
12:45 Nyimbo Na. 5
12:50 FILIMU YAIKULU: Nkhani ya Yona—Kutengapo Phunzilo pa Kulimba Mtima na Cifundo (Yona 1-4)
13:40 Nyimbo Na. 71 na Zilengezo
13:50 Ali ku Mbali Yathu ni Ambili Kuposa Adani Athu! (Deuteronomo 7:17, 21; 28:2; 2 Mafumu 6:16; 2 Mbiri 14:9-11; 32:7, 8, 21; Yesaya 41:10-13)
14:50 Nyimbo na Pemphelo Lothela