LEMBA LA MWEZI: “LALIKILA MAU. LALIKILA MODZIPELEKA.”—2 Tim. 4:2.
Kufotokoza Zimene Timakhulupilila Zokhudza 1914
Malemba amatilimbikitsa ‘kukhala okonzeka kuyankha’ zimene timakhulupilila, “ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambili.” (1 Pet. 3:15) Kunena zoona, nthawi zina zingakhale zovuta kufotokoza mfundo zakuya za coonadi ca m’Baibulo, monga mfundo yokhudza mmene timadziŵila kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila mu 1914. Pofuna kutithandiza kuyankha funso limeneli, pali nkhani ziŵili zimene zingatithandize za mutu wakuti, “Kukambilana Ndi Munthu Wina Nkhani za m’Baibulo—Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulila?” Nkhani zimenezi zipezeka m’magazini a Nsanja ya Mlonda amene tikugaŵila mu ulaliki m’miyezi ya October ndi November. Pamene muŵelenga nkhanizi, ganizilani mafunso otsatilaŵa ndi kuona mmene a Zulu, amene ndi wofalitsa m’nkhaniyo, anayambila makambilano ao.
Ndi motani mmene iye . . .
anayambila makambilano mwa kuyamikila munthu amene anali kuceza naye?—Mac. 17:22.
anaonetsela kudzicepetsa pofotokoza zimene amakhulupilila?—Mac. 14:15.
N’cifukwa ciani iye anacita bwino . . .
kuunikila mwacidule mfundo zimene akambilana asanapite pa mfundo ina?
kuyamba waima ndi kufunsa ngati mwininyumba anali kumvetsa zimene anali kukambilana?
kusafotokoza zambili pa nthawi imodzi?—Yoh. 16:12.
Tiyamikila kwambili Yehova ‘Mlangizi wathu Wamkulu’ potiphunzitsa mmene tingafotokozele bwino ziphunzitso zozama za coonadi ca m’Baibulo kwa amene ali ndi njala yakuuzimu.—Yes. 30:20.