Zida Zathu Zophunzitsila
1. Kodi ofalitsa amafanana bwanji ndi amisili a luso?
1 Amisili aluso amagwilitsila nchito zida zosiyanasiyana. Zina mwa zida zimenezi amazigwilitsila nchito patalipatali malinga ndi nchito imene akugwila, koma zina amazigwilitsila nchito nthawi zonse. Amisili aluso amenewa amakhala ndi zida zofunika kwambili mu bokosi lao la zida makamaka zimene amadziŵa bwino kwambili kuzigwilitsila nchito. Baibulo limalimbikitsa Mkristu aliyense kukhala wodzipeleka mu ulaliki ndi kukhala “wanchito wopanda cifukwa cocitila manyazi.” (2 Tim. 2:15) Kodi ndi cida cofunika kwambili citi cimene tifunika kukhala naco? Ndi Mau a Mulungu, amene ndi cida cacikulu cimene timagwilitsila nchito ‘pophunzitsa anthu.’ (Mat. 28:19, 20) Conco, tiyenela kuyesetsa kukhala aluso “pophunzitsa ndi kufotokoza bwino mau a coonadi.” Komabe pali zida zina zophunzitsila zimene timagwilitsila nchito nthawi zambili, zimene Akristu onse ayenela kudziŵa mmene angazigwilitsile nchito mwaluso pophunzitsa anthu coonadi.—Miy. 22:29.
2. Kodi zida zathu zophunzitsila ndi ziti?
2 Zida Zathu Zophunzitsila: Kupatulapo Baibulo, ndi zida zina ziti zimene tiyenela kugwilitsila nchito? Cida coyambilila cimene tingagwilitsile nchito pophunzitsa anthu ndi buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni. Tikamaliza kuphunzila bukuli ndi wophunzila Baibulo, timayamba kuphunzila naye buku la “Khalanibe M’cikondi ca Mulungu,” n’colinga comuphunzitsa kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo paumoyo wake. Conco tifunika kukhala aluso pogwilitsila nchito zofalitsa zimenezi. Tiyenela kugwilitsilanso nchito tumabuku twina pophunzitsa. Cida cina coyambitsila maphunzilo a Baibulo ndi kabuku ka Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu. Ngati m’gawo lathu muli anthu amene amavutika kuŵelenga kapena amene amalankhula cinenelo cimene tili ndi zofalitsa zocepa kapena tilibiletu m’cineneloco, tingagwilitsile nchito kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu ndi kakuti Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. Cida cina cothandiza potsogolela ophunzila ku gulu, ndi kabuku kakuti Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano? Zida zina zimene tifunika kuphunzila kuzigwilitsila nchito mwaluso ndi mavidiyo monga akuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?, N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? ndi yakuti Does God Have a Name? [Kodi Mulungu Ali ndi Dzina?].
3. Kodi nkhani za mu Utumiki Wathu wa Ufumu za mtsogolo zidzatithandiza kucita ciani?
3 Nkhani za mu Utumiki Wathu wa Ufumu za mtsogolo zidzatithandiza kugwilitsila nchito mwaluso zida zimene tili nazo. Tikamayesetsa kugwilitsila nchito zida zimenezi mwaluso, tidzatsatila malangizo akuti: “Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umacita komanso zimene umaphunzitsa. Pitiliza kucita zimenezi, cifukwa ukatelo udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvela.”—1 Tim. 4:16.