LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 May tsa. 8
  • Mmene Tingaseŵenzetsele JW Laibulale

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Tingaseŵenzetsele JW Laibulale
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mukugwilitsila Nchito JW Laibulale?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Laibulali Imene Mungathe Kuinyamula Kumanja
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Gwilitsilani Nchito Webusaiti ya jw.org mu Ulaliki—“Khala Bwenzi la Yehova”
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Kodi Tingapindule Bwanji ndi Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 May tsa. 8

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Mmene Tingaseŵenzetsele JW Laibulale

POPHUNZILA:

  • Ŵelengani Baibulo ndi kabuku ka kuphunzila Malemba tsiku ndi tsiku.

  • Ŵelengani Buku Lapacaka, magazini, ndi zofalitsa zina. Seŵenzetsani bukumaki.

  • Konzekelani misonkhano yampingo, ndi kuconga mayankho

  • Onelelani mavidiyo

Mboni za Yehova zikuphunzila Baibulo pogwilitsila nchito zipangizo zamakono pamene zili m’coyendela ca onse

PA MISONKHANO:

  • Pezani malemba amene mkambi akuchula. Seŵenzetsani mbali yokuthandizani kupezanso lembalo

  • M’malo monyamula mabuku pobwela kumisonkhano, munganyamule cipangizo canu cokhala ndi intaneti ndi kuciseŵenzetsa pocita misonkhano ndi poimba nyimbo. Pa JW Laibulale pali nyimbo zatsopano zimene m’buku la nyimbo mulibe

Mboni za Yehova zikuseŵenzetsa JW Laibulale pa misonkhano yampingo

MU ULALIKI:

  • Onetsani cinacake munthu wacidwi kucokela pa JW Laibulale, ndiyeno m’thandizeni kucita dawunilodi pulogalamu imeneyi ndiponso zofalitsa zina n’kuziika pa cipangizo cake cokhala ndi intaneti

  • Sewenzetsani mbali yofufuzila kuti mupeze vesi la m’Baibulo. Ngati mau ena ake sakuonekela m’Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso, mungafufuze m’Baibulo lokhala ndi malifalensi

  • Muonetseni vidiyo. Ngati mwininyumba ali ndi ana, mungamuonetse vidiyo imodzi pa mavidiyo akuti Khala Bwenzi la Yehova. Mwina mungamuonetse vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? kuti imupangitse kukhala ndi cidwi ndi phunzilo la Baibulo. Ngati munthu wina amakamba cinenelo cina, muonetseni vidiyo ya m’cinenelo cake

  • Onetsani mwininyumba lemba m’cinenelo cina cimene inu munacita dawunilodi. Pitani pa lembalo ndi kudiniza nambala ya vesi kuti mulinganize zinenelo zonse ziŵili

A Mboni za Yehova akutambitsa vidiyo kwa mtsikana ndi makolo ake
    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani