LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 October tsa. 4
  • Mmene Mungapelekele Mayankho Ogwila Mtima

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Mungapelekele Mayankho Ogwila Mtima
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Nkhani Zofanana
  • Tamandani Yehova Pakati pa Mpingo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Tizilimbikitsana pa Misonkhano ya Mpingo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Mmene Tingakonzekelele Misonkhano Yathu
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 October tsa. 4

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

Mmene Mungapelekele Mayankho Ogwila Mtima

Mnyamata wakweza dzanja pa Phunzilo la Nsanja ya Mlonda, mlongo apeleka ndemang pa Phunzilo la Nsanja ya Mlonda

Mayankho ogwila mtima amalimbikitsa mpingo. (Aroma 14:19) Ndiponso munthu amene wapeleka yankho amapindula. (Miy. 15:23, 28) Conco, tiziyesetsa kukonzekela kuti pa msonkhano uliwonse tizipelekako yankho ngakhale limodzi cabe. Popeza kuti nthawi zina tikanyamula dzanja wocititsa sangatilate, tiyenela kukonzekela ndemanga zingapo.

Yankho logwila mtima . . .

  • limakhala losavuta, lomveka bwino, ndi lalifupi. Kaŵili-kaŵili, yankho la conco lingapelekedwe kwa masekondi 30 kapena ocepelapo

  • muyenela kulipeleka m’mau anu-anu

  • simuyenela kubweleza zimene ena ayankha kale

Ngati ndinu woyamba kupeleka yankho pa funso, . . .

  • pelekani yankho lolunjika na losavuta kumva

Ngati yankho la funso lapelekedwa kale . . .

  • mungafotokoze mmene lemba losagwila mau licilikizila mfundo imene mukambilana

  • fotokozani mmene nkhaniyo ikhudzila umoyo wathu

  • fotokozani mmene tingaseŵenzetsele mfundoyo

  • fotokozani mwacidule citsanzo kapena cocitika cimene cingathandize anthu kumvetsetsa mfundoyo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani