LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 October tsa. 8
  • October 31–November 6

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • October 31–November 6
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mumaseŵenzetsa Makadi Ongenela pa Webusaiti Yathu?
  • Seŵenzetsani Tsamba Loyamba la JW.ORG mu Ulaliki
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Webusaiti Yathu ya JW.ORG
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Kodi Munadzifunsapo?
    Galamuka!—2019
  • Zaka 100 za Ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 October tsa. 8

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

October 31–November 6

Wa Mboni za Yehova agaŵila munthu khadi yongenela pa Webusati yathu

Kodi Mumaseŵenzetsa Makadi Ongenela pa Webusaiti Yathu?

Nchito yolalikila ifunika kucitika mwamsanga cifukwa cisautso cacikulu cayandikila. (Miy. 24:11, 12, 20) Tingaseŵenzetse makadi ongenela pa webusaiti yathu kuti tithandize anthu kucita cidwi na Mau a Mulungu ndi webusaiti yathu. Khadi imeneyi ili na QR khodi yooneka monga kacidindo yopezela vidiyo yakuti, N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? QR khodi imeneyi ingathandize munthu kudziŵa zambili, ngakhale kupempha phunzilo la Baibulo. Pali anthu ena amene amakana zofalitsa zathu, koma amalola kupita pa webusaiti yathu. Anthu a conco tiyenela kuwapatsa makadi amenewa. Komabe, musawagaŵile kwa anthu amene alibe cidwi.

Pa zocita za tsiku na tsiku, mungayambe kukambilana na munthu mwa kukamba kuti: “Nili na kanthu kena kamene nifuna kukupatsani. Ni khadi yongenela pa webusaiti imene ili na mavidiyo na nkhani zosiyana-siyana zimene mungaŵelenge.” (Yoh. 4:7) Popeza kuti makadi amenewa ni ang’ono-ang’ono, mukhoza kuwanyamula kuti pakapezeka mpata muzigaŵilako ena.

GAŴILANI KHADI IMENEYI. . .

  • mu ulaliki wamwayi

  • mu ulaliki wa m’gawo la malonda

  • kwa anthu amene amamvetsela uthenga wathu koma amakana zofalitsa

Khadi yongenela pa Webusati yathu yoonetsa Baibo yotsegula
Khadi yongenela pa Webusati yathu yoonetsa wa Mboni za Yehova aŵelengela Baibo munthu wina
Khadi yongenela pa Webusati yathu yoonetsa wa Mboni za Yehova acita phunzilo la Baibo na banja lina
Kumbuyo kwa khadi yongenela pa Webusati yathu

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani