LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 September tsa. 16
  • Seŵenzetsani Tsamba Loyamba la JW.ORG mu Ulaliki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Seŵenzetsani Tsamba Loyamba la JW.ORG mu Ulaliki
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Mfundo Yothandiza Yokhudza Webusaiti Yathu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Kodi Munadzifunsapo?
    Galamuka!—2019
  • Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • October 31–November 6
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 September tsa. 16
Zithunzi zoonetsa nkhani zopezeka pa tsamba loyamba la jw.org mu zinenelo zosiyanasiyana.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Seŵenzetsani Tsamba Loyamba la JW.ORG mu Ulaliki

Pa tsamba loyamba la webusaiti yathu pamapezeka nkhani na mavidiyo amene anakonzedwa kuti azikopa cidwi ca anthu oona mtima amene si Mboni. (Mac. 13:48) Nthawi zambili pa tsambali pamakhala nkhani zimene zafalitsidwa pa nyuzi kapena zimene zili m’kamwa-m’kamwa.

Kodi mungaliseŵenzetse bwanji tsamba loyamba la webusaiti yathu mu ulaliki?

  • Muzionapo kaŵili-kaŵili pa webusaiti yathu. Onani nkhani zimene zili pansi pa kamutu kakuti “Zimene Zilipo” na kuganizila mmene mungaziseŵenzetsele polalikila munthu wacidwi. (Kuti mupeze nkhani zina zimene zinali pa tsamba loyamba caposacedwa, dinizani pa “Onani Zina.”) Mukamaonapo kaŵili-kaŵili pa webusaiti yathu mudzapeza mfundo zatsopano zoseŵenzetsa mu ulaliki.

  • Gwilitsani nchito nkhani na mavidiyo opezeka pa tsamba loyamba poyambitsa makambilano. Mavidiyo na nkhani zimenezi zidzakuthandizani kudziŵa zimene anthu a m’dela lanu akuganizila.

  • Onetsani anthu tsamba loyamba la webusaiti yathu. Pokambilana na munthu, muunikilen’koni nkhani zina pa tsambalo komanso muonetseni mmene angapezele zinthu pa webusaiti yathu.

  • Tumizani linki. Anthu ena safuna kukamba nafe pamaso-m’pamaso koma amavomela kupita pa webusaiti yathu. Conco, musazengeleze kutumizila munthu wacidwi linki ya tsamba loyamba la webusaiti yathu kapena ya nkhani inayake pa tsambalo, kapenanso ya vidiyo ili pamenepo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani