CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 17-18
Tengelani Citsanzo ca Mtumwi Paulo Polalikila na Kuphunzitsa
17:2, 3, 17, 22, 23
Tingatengele bwanji citsanzo ca mtumwi Paulo?
Tiziseŵenzetsa Malemba pokambilana na anthu, komanso kuwafotokoza mogwilizana na omvela athu
Tizilalikila kumene kumapezeka anthu, komanso pa nthawi yoyenela
Mosamala tizipewa kutsutsa zimene ena amakhulupilila n’colinga cakuti tiyale maziko abwino a ulaliki