CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 17–18
Amuna Odzicepetsa Amaphunzitsa Ena Nchito na Kuwagaŵila Maudindo
18:17, 18, 21, 22, 24, 25
Abale amene ni aciyamba kale, angaonetse kudzicepetsa, cikondi, komanso kuzindikila, pamene aphunzitsa nchito anyamata na kuwagawila maudindo. Motani?
Sankhani abale amene angathe kusenza maudindo owonjezeleka m’gulu la Yehova
Afotokozeleni momveka bwino zimene ayenela kucita kuti aigwile bwino nchitoyo
Apatseni ndalama, zida, komanso thandizo limene angafunike kuti agwile nchitoyo
Muziona mmene m’baleyo akugwilila nchito, na kumuuza kuti muli na cidalilo coti adzaigwila bwino nchitoyo
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ni maudindo ena ati amene ningapatseko ena?’