LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb19 December tsa. 7
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Khalani Okonzeka Kusintha Ulaliki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Khalani Okonzeka Kusintha Ulaliki
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Nkhani Zofanana
  • Muzionetsa Khalidwe Lopambana mu Ulaliki
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kugaŵila Buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Seŵenzetsani Nkhani Zongocitika Kumene mu Ulaliki
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Mmene Tingayankhile Anthu Amene Safuna Kuti Tikambitsilane Nao
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
mwb19 December tsa. 7
Alongo aŵili akuseŵenzetsa tabuleti polalikila woyang’anila famu ya ziŵeto

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki​—Khalani Okonzeka Kusintha Ulaliki

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Odzozedwa komanso a nkhosa zina amaitanila anthu kuti “amwe madzi a moyo kwaulele.” (Chiv. 22:17) Madzi ophiphilitsila amenewa aimila zinthu zonse zimene Yehova wapeleka kuti zipulumutse anthu omvela ku ucimo na imfa. Kuti tithandize anthu kucoka ku miyambo yawo na zikhulupililo za cipembedzo cawo, tifunika kulalikila “uthenga wabwino” m’njila yakuti uziwafika pamtima.—Chiv. 14:6

MMENE TINGACITILE:

  • Sankhani nkhani na lemba limene lingafike pamtima anthu m’gawo lanu. Mungasankhe makambilano acitsanzo kapena nkhani ina imene munagwilitsapo nchito, imene inali na zotulukapo zabwino. Kodi anthu amacita cidwi na nkhani ziti ndiponso malemba ati? Kodi pali nkhani ya pa nyuzi imene anthu ambili akukambapo? Ni nkhani ziti zimene zingakope akazi kapena amuna?

  • Pokambilana na anthu, muziwapatsa moni komanso muzicita zinthu mogwilizana na cikhalidwe ca kwanuko.—2 Akor. 6:3, 4

  • Zidziŵeni bwino zofalitsa na mavidiyo a mu Thuboksi yathu Yophunzitsila kuti mugaŵaleko munthu amene angaonetse cidwi

  • Citani daunilodi zofalitsa za m’citundu ca anthu amene mungakumane nawo m’gawo lanu.

  • Sinthani ulaliki wanu kuti ukhale wogwilizana na zosoŵa za mwininyumba. (1 Akor. 9:19-23) Mwacitsanzo, kodi mungakambe ciani ngati mwadziŵa kuti posacedwa mwininyumba anataikilidwa wokondedwa wake mu imfa?

TAMBITSANI VIDIYO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi wofalitsa anayamba kukambilana nkhani yanji na mwininyumba?

  • Kodi mwininyumba anakumana na mavuto otani mu umoyo wake?

  • Ni lemba liti limene likanagwilizana bwino na cocitikaco? Nanga n’cifukwa ciani?

  • Mungasinthe bwanji ulaliki wanu kuti ukhale wokopa kwa anthu a m’gawo lanu?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani