CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 8-9
Farao Wonyadayo Mosadziŵa Anathandiza Kuti Cifunilo ca Mulungu Cikwanilitsidwe
8:15, 18, 19; 9:15-17
Afarao a ku Iguputo anali kudziona monga milungu. Izi zitithandiza kumvetsa cifukwa cake Farao anali wonyada kwambili kuti amvele Mose na Aroni, komanso kuti amvele ansembe ake ocita zamatsenga.
Kodi mumakhala wokonzeka kumvela malingalilo a ena? Kodi mumayamikila ena akakupatsani uphungu? Kapena kodi nthawi zonse mumadziona kuti ndimwe wosalakwa? Baibo imati: “Kunyada kumafikitsa munthu ku ciwonongeko.” (Miy. 16:18) Conco tifunika kupewalatu khalidwe la kunyada!