CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 21-22
Muzionetsa kuti Mumaona Moyo Mmene Yehova Amauonela
21:20, 22, 23, 28, 29
Yehova amaona moyo kukhala wamtengo wapatali. Kodi tingaonetse bwanji kuti timaona moyo mmene iye amauonela?
Muzikonda kwambili anthu ena na kuwalemekeza.—Mat. 22:39; 1 Yoh. 3:15
Onetsani cikondi cimeneco mwa kuwonjezela cangu canu mu ulaliki.—1 Akor. 9:22, 23; 2 Pet. 3:9
Muziona nkhani ya citetezo kukhala yofunika kwambili.—Miy. 22:3
Kodi kulemekeza moyo n’kogwilizana bwanji na kukhala wopanda mlandu wa magazi?