LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 July tsa. 11
  • Mungathandize Kuti m’Banja Lanu Mukhale Cimwemwe

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mungathandize Kuti m’Banja Lanu Mukhale Cimwemwe
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Banja Lanu Lingakhalile Lacimwemwe
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Cilango Cimaonetsa Cikondi ca Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Seŵenzetsani Mfundo za m’Baibo Pothandiza Ana Anu Kuti Apambane
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Uzilemekeza Atate Ako ndi Amayi Ako
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 July tsa. 11
Zithunzi: Zithunzi zozikika pa vidiyo yakuti “Kulitsani Cimwemwe m’Banja Lanu.” 1. Atsikana akuona makolo awo pamene akudya keke. 2. Atsikanawo akuseka pa kulambila kwa pa banja. 3.Mmodzi mwa atsikanawo akuona amayi ake odwala amene agona pa sofa.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Mungathandize Kuti m’Banja Lanu Mukhale Cimwemwe

Yehova amafuna kuti anthu m’banja azikhala acimwemwe. (Sal. 127:3-5; Mlal. 9:9; 11:9) Komabe, tingataye cimwemwe cathu cifukwa ca mavuto a m’dzikoli, komanso cifukwa ca zophophonya za a m’banja lathu. Kodi aliyense angacite ciyani kuti m’banja lawo mukhale cimwemwe?

Mwamuna ayenela kupatsa ulemu mkazi wake. (1 Pet. 3:7) Ayenela kumapeza nthawi yoceza naye. Asamamuyembekezele kucita zimene sangakwanitse, ndipo azionetsa kuti amayamikila zimene amamucitila komanso zimene amacitila banja lawo. (Akol. 3:15) Azimuonetsa cikondi na kum’tamanda.—Miy. 31:28, 31.

Mkazi ayenela kufuna-funa njila zothandizila mwamuna wake. (Miy. 31:12) Azigonjela mwamuna wake na kugwilizana naye pocita zinthu. (Akol. 3:18) Azikamba zabwino za iye na kulankhula naye mokoma mtima.—Miy. 31:26.

Makolo ayenela kumapatula nthawi yoceza na ana awo. (Deut. 6:6, 7) Komanso aziwauza kuti amawakonda. (Mat. 3:17) Ndipo powapatsa cilango, azicita nawo mwacikondi komanso mozindikila.—Aef. 6:4.

Ana ayenela kulemekeza makolo awo na kuwamvela. (Miy. 23:22) Azimasuka kufotokozela makolo awo zimene akuganiza komanso mmene akumvela. Azimvela uphungu na ulangizi wa makolo awo, ndipo azionetsa kuti amawalemekeza makolowo.—Miy. 19:20.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KULITSANI CIMWEMWE M’BANJA LANU, KENAKO YANKHANI FUNSO ILI:

Kodi aliyense wa anthu a mu vidiyo imeneyi anacita ciyani kuti akulitse cimwemwe m’banja lawo?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani