LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 January tsa. 11
  • Acinyamata—Auzeni za Mumtima Mwanu Makolo Anu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Acinyamata—Auzeni za Mumtima Mwanu Makolo Anu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Uzilemekeza Atate Ako ndi Amayi Ako
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Mungathandize Kuti m’Banja Lanu Mukhale Cimwemwe
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Inu Makolo—Thandizani Ana Anu Kukonda Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 2
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 January tsa. 11

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Acinyamata—Auzeni za Mumtima Mwanu Makolo Anu

N’cifukwa ciani muyenela kumasuka kuuza makolo anu za mumtima mwanu? (Miy. 23:26) Cifukwa Yehova anawapatsa udindo wokusamalilani na kukutsogolelani. (Sal. 127:3, 4) Cingakhale covuta kwa iwo kukuthandizani ngati simuwafotokozela nkhawa zanu zonse. Komanso mungataye mwayi wopindula na nzelu zimene apeza pa umoyo wawo. Koma kodi n’kulakwa kusawafotokozelako zina zimene mukuganiza? Osati kwenikweni—malinga ngati simukucita zinthu zaciphamaso.—Miy. 3:32.

Kodi mungakambe nawo bwanji makolo anu? Yesani kupeza nthawi yabwino kwa inu na iwo. Ngati zimenezo n’zovuta, mungalembele kalata mmodzi wa makolo anu yowauzako za mumtima mwanu. Nanga bwanji ngati afuna kuti mukambilane nawo nkhani imene inu sindinu omasuka kuikambilana? Kumbukilani kuti iwo amafunitsitsa kukuthandizani. Muziwaona kuti ni mabwenzi anu, osati adani anu. Ngati muyesetsa kukambilana momasuka na makolo anu, mudzapindula kwa moyo wanu wonse, inde kwamuyaya.—Miy. 4:10-12.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI UMOYO WANGA NILI WACICEPELE—KODI NINGAKAMBE NAWO BWANJI MAKOLO ANGA? KENAKO KAMBILANANI MAFUNSO AWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Umoyo Wanga Nili Wacicepele—Kodi Ningakambe Nawo Bwanji Makolo Anga?” Mtsikana wovala ma hedifoni akuseŵenzetsa kompyuta, ndipo akunyalanyaza amayi ake amene afuna kukamba naye.

    Kodi Esther na Partik anazindikila ciani zokhudza umoyo wawo?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Umoyo Wanga Nili Wacicepele—Kodi Ningakambe Nawo Bwanji Makolo Anga?” Mtsikana akukamba na amayi ake, ndipo akuwaonetsa zinazake pa foni yake.

    Mungaphunzile ciani pa citsanzo ca Yesu?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Umoyo Wanga Nili Wacicepele—Kodi Ningakambe Nawo Bwanji Makolo Anga?” Mayi walekeza kugwila nchito zake zapanyumba kuti aseŵeleko na mwana wake wamng’ono.

    Kodi makolo anu aonetsa bwanji kuti amakukondani?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Umoyo Wanga Nili Wacicepele—Kodi Ningakambe Nawo Bwanji Makolo Anga?” Koci wa maseŵela a basketball akujambula zithunzi zoonetsa mmene timu yake iyenela kucitila maseŵelawo.

    Makolo anu amafuna kuti zinthu zizikuyendelani bwino

    Ni mfundo za m’Baibo ziti zimene zingakuthandizeni kuti muzikambilana na makolo anu?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani