Davide wayang’anizana na Goliyati
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”
Cikhulupililo ca Davide mwa Yehova cinali cozikidwa pa zimene anaphunzila na zimene zinamucitikila pa umoyo (1 Sam. 17:36, 37; wp16.5 11 ¶2-3)
Davide sanadziyelekezele na Goliyati, koma anayelekezela Goliyati na Yehova (1 Sam. 17:45-47; wp16.5 11-12)
Yehova anathandiza Davide kugonjetsa mdani wamphamvu komanso woopsa (1 Sam. 17:48-50; wp16.5 12 ¶4; onani cithunzi ca pacikuto)
Nthawi zina, tingakhale na zopinga zazikulu monga cizunzo kapena cizoloŵezi coipa. Ngati tiona kuti mavuto athu ni aakulu kwambili, tizikumbukila kuti ni aang’ono tikawayelekezela na mphamvu zopanda malile za Yehova.—Yobu 42:1, 2.