Mfumu Solomo akuona mmene nchito yomanga kacisi ikuyendela
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Anagwila Nchito Molimbika Cifukwa Cokonda Yehova
Solomo anagwilitsa nchito zipangizo zabwino kwambili pomanga kacisi (1 Maf. 5:6, 17; w11 2/1 15)
Anthu ambili anagwilako nchitoyo (1 Maf. 5:13-16; it-1 424; it-2 1077 ¶1)
Solomo na anthuwo anagwila nchito molimbika kwa zaka 7 kuti amalize kumanga kacisi (1 Maf. 6:38; onani cithunzi ca pacikuto)
Cifukwa cokonda Yehova, Solomo na anthuwo anamanga kacisi wokongola amene anapangitsa kuti Yehova atamandike. Koma cacisoni n’cakuti, mibadwo ya m’tsogolo mwawo inalibe cangu pa kulambila koona. Iwo analeka kusamalila kacisiyo, ndipo pambuyo pake kacisiyo anawonongedwa.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nikucita ciyani kuti nikhalebe wokangalika polambila Yehova?’