CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Muziyang’ana kwa Yehova Kuti Mupeze Citonthozo
Eliya anacita mantha, ndipo anathaŵa kuti apulumutse moyo wake (1 Maf. 19:3, 4; w19.06 15 ¶5)
Yehova anam’patsa thandizo lofunikila na kumuonetsa mphamvu zake zocititsa mantha (1 Maf. 19:5-7, 11, 12; ia 103 ¶13; 106 ¶21)
Yehova anapatsa Eliya nchito yakuti agwile (1 Maf. 19:15-18; ia 106 ¶22)
Masiku ano, Yehova amakamba nafe kupitila m’Mawu ake, Baibo. Iye amatikumbutsa kuti amatikonda kwambili, ndipo watipatsa nchito yabwino yoti tizigwila.—1 Akor. 15:58; Akol. 3:23.