LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 January tsa. 11
  • Fufuzani Kuti Mudziŵe Maganizo a Mulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Fufuzani Kuti Mudziŵe Maganizo a Mulungu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Pangani Zisankho Zokondweletsa Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Kufuna-funa Nzelu mwa Kuŵelenga Baibo Tsiku Lililonse
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kukondweletsa Mulungu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 January tsa. 11
Cithunzi cocokela mu vidiyo yakuti “Tifunika “Kuthamanga Mopilila”—Idyani Zakudya Zopatsa Thanzi.” Mlongo Rebekah akufufuza pogwilitsa nchito bulosha yakuti “Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri”.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Fufuzani Kuti Mudziŵe Maganizo a Mulungu

Timafuna kukondweletsa Yehova m’zocita zathu zonse. (Miy. 27:11) Koma kuti ticite zimenezi, tiyenela kupanga zisankho zogwilizana na maganizo ake, ngakhale kuti palibe lamulo lacindunji lotitsogolela pankhaniyo. Kodi n’ciyani cingatithandize kucita zimenezi?

Muziŵelenga Baibo nthawi zonse. Nthawi zonse tikamaŵelenga Baibo, zimakhala ngati tikuceza na Yehova. Tingadziŵe maganizo a Yehova mwa kuona mmene anacitila zinthu na anthu ake komanso kusinkhasinkha zitsanzo za anthu amene anacita zabwino kapena zoipa pamaso pake. Tikafuna kupanga cisankho, mzimu woyela ungatithandize kukumbukila mfundo zofunika zimene tinaphunzila m’Mawu a Mulungu.—Yoh. 14:26.

Fufuzani. Mukafuna kupanga cisankho, dzifunseni kuti, ‘Kodi ni mavesi ati kapena zocitika ziti zochulidwa m’Baibo zimene zinganithandize kumvetsa mmene Yehova amaonela nkhaniyi?’ Pemphani thandizo kwa Yehova, ndipo seŵenzetsani zida zofufuzila zimene zilipo m’cinenelo canu kuti zikuthandizeni kupeza mfundo za m’Baibo. Zidazo zingakuthandizeninso kuona mmene mungagwilitsile nchito mfundozo popanga cisankho canu.—Sal. 25:4.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI TIFUNIKA “KUTHAMANGA MOPILILA”—IDYANI ZAKUDYA ZOPATSA THANZI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Ni mavuto otani amene mlongo wacitsikana wa m’vidiyoyi anakumana nawo?

  • Kodi mungaseŵenzetse bwanji zida zofufuzila kuti zikuthandizeni kulimbana na mavuto monga amene mlongoyu anakumana nawo?

  • Kodi timapindula bwanji ngati tipatula nthawi yofufuza na kucita phunzilo la munthu mwini kuti tipeze mfundo zotithandiza kupanga zisankho zabwino?—Aheb. 5:13, 14

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani