UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kukondweletsa Mulungu
Yehova amaona kuti acicepele ni amtengo wapatali. Iye amaona mmene amapitila patsoglo mwauzimu komanso zimene amapilila. (1 Sam. 2:26; Luka 2:52) Ngakhale atakhala kuti ni acicepele kwambili, ana angakondweletse mtima wa Yehova mwa khalidwe lawo labwino. (Miy. 27:11) Mwa gulu lake, Yehova wapeleka zida zabwino kwambili zothandiza makolo kuphunzitsa ana awo kuti azikonda Yehova na kumumvela.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI ACICEPELE—YEHOVA AMAKONDWELA MUKAMAPILILA! KENAKO YANKHANI MAFUNSO AYA:
Kwa zaka, kodi Yehova wakhala akupeleka malangizo otani othandiza acicepele?
Kodi pali zida zotani zothandiza makolo kuphunzitsa ana?
Ngati ndinu wacicepele, kodi Yehova wakupatsani ciyani cimene cakupindulilani? Nanga mwapindula motani?