UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zimene Ningacite Kuti Niteteze Mbili Yabwino ya Gulu Lathu
Anthu amaona khalidwe la Mboni za Yehova. (1 Akor. 4:9) Tingadzifunse kuti, ‘Kodi zokamba na zocita zanga zimapeleka ulemelelo kwa Yehova?’ (1 Pet. 2:12) Mosakayikila, sitifuna kucita ciliconse cimene cingawononge mbili yabwino imene Mboni za Yehova zakhala nayo kwa zaka zambili.—Mlal. 10:1.
Pa zocitika zotsatilazi, lembani zimene Mkhristu ayenela kucita komanso mfundo yothandiza ya m’Baibo:
Munthu amene si Mboni wakunyozani mwaukali
Zovala zanu, motoka, kapena nyumba yanu n’zakuda
Lamulo la boma silinakukomeleni kapena n’lovuta kulitsatila
Kodi ofufuza a m’Dipatimenti Yolemba Mabuku amacita ciyani kuti tikhalebe na mbili yabwino?
TAMBANI VIDIYO YAKUTI TIMAKONDA NA KULEMEKEZA COONADI, KENAKO YANKHANI FUNSO ILI:
N’ciyani cakukondweletsani poona zimene gulu lathu limacita kuti likonze nkhani zolondola?