NYIMBO 142
Tigwilitsitse Ciyembekezo Cathu
Yopulinta
	(Aheberi 6:18, 19)
- 1. Zaka zambili-mbili anthu pa dziko - Adzandiladi mosaphula kanthu. - Mwacisoni ali mu ukapolo - Cifukwa onse ni ocimwa. - (KOLASI) - Ufumu wa Mulungu wafika! - Khristu adzatimasula ku mantha. - Posacedwa zoipa zidzatha. - Ciyembekezoci citilimbitsa. 
- 2. Tsiku la Yehova M’lungu layandika! - Anthu sadzalilanso: “Mpaka liti?” - Yehova ‘dzamasula cilengedwe. - Tim’tamande ndipo tiimbe. - (KOLASI) - Ufumu wa Mulungu wafika! - Khristu adzatimasula ku mantha. - Posacedwa zoipa zidzatha. - Ciyembekezoci citilimbitsa. 
(Onaninso Sal. 27:14; Mla. 1:14; Yow. 2:1; Hab. 1:2, 3; Aroma 8:22.)