NYIMBO 58
Kusakila Anthu Okonda Mtendele
Yopulinta
1. Yesu anati: ‘Lalikilani.’
Paliponse, kulikonse, Iye analalikila.
Anasakila nkhosa za M’lungu
Mpaka kuloŵa kwa dzuŵa ‘nasakilabe.
Mu makomo na m’misewu,
Tilalikila ‘liyense
Tiuza anthu: “Mavuto adzatha.”
(KOLASI)
Tisakila
A mtendele m’mitundu yonse.
Tisakila
Ofunadi cipulumutso,
Sitisiya
Aliyense.
2. Nthawi ikutha, ticite cangu.
Tisakile, tifufuze, Tipulumutseko ena.
Cifukwa timaŵakonda anthu.
Timabwelelako na mau otonthoza.
Mu midzi na m’matauni
Tisakila omvetsela,
Ndipo tikaŵapeza timakondwa.
(KOLASI)
Tisakila
A mtendele m’mitundu yonse.
Tisakila
Ofunadi cipulumutso,
Sitisiya
Aliyense.
(Onaninso Yes. 52:7; Mat. 28:19, 20; Luka 8:1; Aroma 10:10.)