NYIMBO 142
Tigwilitsitse Ciyembekezo Cathu
Yopulinta
(Aheberi 6:18, 19)
1. Zaka zambili-mbili anthu pa dziko
Adzandiladi mosaphula kanthu.
Mwacisoni ali mu ukapolo
Cifukwa onse ni ocimwa.
(KOLASI)
Ufumu wa Mulungu wafika!
Khristu adzatimasula ku mantha.
Posacedwa zoipa zidzatha.
Ciyembekezoci citilimbitsa.
2. Tsiku la Yehova M’lungu layandika!
Anthu sadzalilanso: “Mpaka liti?”
Yehova ‘dzamasula cilengedwe.
Tim’tamande ndipo tiimbe.
(KOLASI)
Ufumu wa Mulungu wafika!
Khristu adzatimasula ku mantha.
Posacedwa zoipa zidzatha.
Ciyembekezoci citilimbitsa.
(Onaninso Sal. 27:14; Mla. 1:14; Yow. 2:1; Hab. 1:2, 3; Aroma 8:22.)