NYIMBO 61
Patsogolo! Inu Mboni Zake
- 1. Mboni za Yehova n’zolimba mtima - Zimalengeza Ufumu wa Yehova. - Ngakhale Satana ‘zizunze, - Sizileka, zidalila Yehova. - (KOLASI) - Imwe Mboni za M’lungu, limbani mtima! - Tumikilani Yehova na cimwemwe! - Uzani onse kuti omvela M’lungu - Adzakhala m’dziko latsopano. 
- 2. Atumiki a Yehova Mulungu, - Sacita mantha polalikila anthu. - Samakonda zinthu za m’dziko; - Iwo saiŵala Mulungu wao. - (KOLASI) - Imwe Mboni za M’lungu, limbani mtima! - Tumikilani Yehova na cimwemwe! - Uzani onse kuti omvela M’lungu - Adzakhala m’dziko latsopano. 
- 3. Anthu amanyoza dzina la M’lungu. - Samalemekeza ucifumu wake. - Tiyeni’se tiwacenjeze; - Tidziŵikitse dzina la Yehova. - (KOLASI) - Imwe Mboni za M’lungu, limbani mtima! - Tumikilani Yehova na cimwemwe! - Uzani onse kuti omvela M’lungu - Adzakhala m’dziko latsopano. 
(Onaninso Eks. 9:16; Afi. 1:7; 2 Ti. 2:3, 4; Yak. 1:27.)