NYIMBO 22
Ufumu Ulamulila—Ubwele!
Yopulinta
	(Chivumbulutso 11:15; 12:10)
- 1. Yehova Mulungu wathu, - Ndimwe wamuyaya - Mwalonga Yesu ufumu; - Mwa kufuna kwanu. - Khristu akulamulila; - Adzalamulila konse. - (KOLASI) - Lomba zafikadi - Cipulumutso, na mphamvu. - Ufumu wabadwa. - Timapemphela: “Ubwele!” 
- 2. Satana ‘dzaonongedwa - Kwatsala pang’ono. - Ise tingasautsike - Koma timadziŵa: - Khristu akulamulila - Adzalamulila konse. - (KOLASI) - Lomba zafikadi - Cipulumutso, na mphamvu. - Ufumu wabadwa. - Timapemphela: “Ubwele!” 
- 3. Angelo asekelela - Aimba mokondwa. - Satana n’ziŵanda zake - Anagonjetsedwa. - Khristu akulamulila; - Adzalamulila konse. - (KOLASI) - Lomba zafikadi - Cipulumutso, na mphamvu. - Ufumu wabadwa. - Timapemphela: “Ubwele!” 
(Onaninso Dan. 2:34, 35; 2 Akor. 4:18.)