NYIMBO 64
Timasangalala Kuthandizila pa Nchito Yokolola
Yopulinta
1. Ino ni nthawi yokolola,
Ni mwayi wosangalatsa.
Onani mindayo yayela,
Tiyeni ticite cangu.
Yesu amatitsogolela,
Pamene tilalikila.
Timayamikila nchito iyi,
Timaicita mokondwa.
2. Tigwile nchitoyi mwakhama,
Pokonda anthu na M’lungu.
Tiphunzitse onse mwam’sanga,
Mapeto ayandikila.
Cimwemwe cimene tipeza,
N’dalitsodi la Yehova.
Tigwile nchitoyi mosaleka,
M’lungu adzatidalitsa.
(Onaninso Mat. 24:13; 1 Akor. 3:9; 2 Tim. 4:2.)