Kugwilitsila Nchito Kabuku ka Uthenga Wabwino Pophunzitsa
1. Kodi kabuku ka Uthenga Wabwino kanalembedwa bwanji?
1 Monga mmene tinaphunzilila mu Utumiki wathu wa Ufumu, wa July, cimodzi mwa zida zofunika pophunzitsa ndi kabuku ka Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu. Malemba ena sanagwidwe mau n’colinga cakuti eninyumba azipindula ndi phunzilo mwa kuŵelenga malemba m’Baibulo lenilenilo. Ngakhale kuti zofalitsa zathu zimalembedwa m’njila yakuti munthu angamvetsetse coonadi popanda wom’thandiza, kabukuka kanalembedwa m’njila yakuti munthu aziphunzitsidwa ndi wina wake. Conco, tikagaŵila kabukuka, tiyenela kuonetsa mwininyumba mmene timacitila phunzilo la Baibulo kuti aone mmene kuphunzila uthenga wabwino wocokela m’Baibulo kumasangalatsila.—Mat. 13:44.
2. Tingagwilitsile nchito bwanji kabuku ka Uthenga Wabwino pa ulendo woyamba?
2 Paulendo Woyamba: Mungakambe kuti: “Ndabwela pano cifukwa ambili amada nkhawa akaganizila za tsogolo la anthu. Kodi muganiza kuti zinthu zidzakhala bwanji mtsogolo? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo lili ndi uthenga wabwino umene umatipatsa ciyembekezo. Pano pali mafunso ena amene Baibulo limayankha.” M’patseni mwininyumba kabuku kameneka, ndiyeno m’pempheni kuti asankhe funso pa mafunso amene ali kucikuto cothela. Pambuyo pake, muonetseni mmene phunzilo la Baibulo limacitikila mwa kuŵelenga ndime imodzi pa nkhani imene wasankha. Njila ina ndi kufunsa mwininyumba funso locititsa cidwi locokela m’nkhani imene inu mwasankha, ndiyeno muonetseni mmene kabukuka kangam’thandizile kupeza mayankho a m’Baibulo. Ngati pa jw.org pali vidiyo yogwilizana ndi nkhani imene wasankhayo, ofalitsa ena amamuonetsa pokambilana naye.
3. Fotokozani mmene tingagwilitsile nchito kabuku ka Uthenga Wabwino pocititsa phunzilo la Baibulo.
3 Mmene Tingacititsile Phunzilo la Baibulo: (1) Ŵelengani funso limene lili m’zilembo zakuda kuti muthandize mwininyumba kuika maganizo ake pa mfundo yaikulu. (2) Ŵelengani ndime ya munsi mwa funsolo. (3) Ŵelengani malemba amene ali m’zilembo zopendeka, ndiyeno funsani mafunso mwaluso kuti muthandize mwininyumba kuona mmene malemba akuyankhila funso limenelo. (4) Ngati munsi mwa funsolo muli ndime ina, tsatilani njila yaciŵili ndi yacitatu. Ngati vidiyo igwilizana ndi funso ndipo simunamuonetsepo vidiyo imeneyi mungamuonetse pamene mukukambilana. (5) Pomaliza, funsani mwininyumba funso limene lili m’zilembo zakuda kuti mudziŵe ngati wamvetsa zimene mwaphunzila naye.
4. N’ciani cingatithandize kugwilitsila nchito mwaluso cida cofunika kwambili cimeneci?
4 Cidziŵeni bwino cida cophunzitsila cimeneci. Muzicigwilitsila nchito pa mpata uliwonse umene wapezeka. Pokonzekela phunzilo lililonse, muziganizila wophunzila wanu ndi mmene mungakambilane naye ndipo muziŵelenga malemba amene ali m’nkhaniyo. (Miy. 15:28; Mac. 17:2, 3) Mukapitiliza kukaseŵenzetsa mwaluso, mudzakakonda kwambili ndipo mudzafuna kukagwilitsila nchito nthawi zonse pophunzitsa ena coonadi.