LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr19 February masa. 1-5
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2019
  • Tumitu
  • FEBRUARY 4-10
  • FEBRUARY 11-17
  • FEBRUARY 18-24
  • FEBRUARY 25–MARCH 3
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2019
mwbr19 February masa. 1-5

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

FEBRUARY 4-10

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 1-3

“Pitilizani Kuphunzitsa Cikumbumtima Canu”

lv peji 16 pala. 6

Mmene Mungasungile Cikumbumtima Cabwino

6 Kodi ndi atumiki a Yehova okha amene ali ndi mphatso ya cikumbumtima? Ganizilani mawu ouzilidwa a mtumwi Paulo akuti: “Nthawi zonse anthu a mitundu amene alibe cilamulo akamacita mwacibadwa zinthu za m’cilamulo, amakhala cilamulo kwa iwo eni ngakhale kuti alibe cilamulo. Amenewa ndiwo amasonyeza kuti mfundo za m’cilamulo zinalembedwa m’mitima mwawo, pamene cikumbumtima cawo cimacitila umboni pamodzi ndi iwowo, ndipo maganizo awo amawatsutsa ngakhalenso kuwavomeleza.” (Aroma 2:​14, 15) Ngakhale anthu amene sadziŵa malamulo a Yehova, nthawi zina amacita zinthu zogwilizana ndi mfundo za Mulungu cifukwa ca cikumbumtima cawo.

lv mape. 17-18 mapa. 8-9

Mmene Mungasungile Cikumbumtima Cabwino

8 Kodi mumapanga bwanji zosankha potsatila cikumbumtima canu? Ena amangoyang’ana pa zimene iwo akuganiza, zimene mtima wawo ukufuna, basi n’kupanga cosankha. Anganene kuti, “Koma cikumbumtima canga sicikunditsutsa.” Zokhumba za mtima zingakhale zamphamvu kwambili cakuti zingapondeleze cikumbumtima. Baibulo limakamba kuti: “Mtima ndi wonyenga kwambili kuposa cina ciliconse ndipo ungathe kucita cina ciliconse coipa. Ndani angaudziŵe?” (Yeremiya 17:⁠9) Conco, tisamangotsatila zimene mtima wathu ukufuna. M’malo mwake, tiyenela kuona cimene cingakondweletse Yehova Mulungu.

9 Ngati cosankha cathu cizikidwa pa cikumbumtima cathu cophunzitsidwa bwino, cosankhaco cidzaonetsa kuti timaopa Mulungu m’malo motsatila zofuna zathu. Taganizilani citsanzo cabwino ici cokhudza nkhani imeneyi. Bwanamkubwa wokhulupilika Nehemiya anali ndi ufulu wolamula anthu a ku Yerusalemu kuti azikhoma misonkho yosiyanasiyana kwa iye. Koma iye sanacite zimenezo. Cifukwa ciani? Iye sanafune kukwiyitsa Yehova ngakhale pang’ono mwa kuika mtolo pa anthu a Mulungu. Iye anati: “Koma ine sindinacite zimenezo cifukwa coopa Mulungu.” (Nehemiya 5:15) Inde, kuopadi Mulungu, kapena kuti kuopa kukhumudwitsa Atate wathu wakumwamba, n’kofunika kwambili. Kuopa Mulungu kwa conco, kudzatithandiza kufuna citsogozo ca Mawu ake popanga zosankha.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w08 6/15 peji 30 pala. 5

Mfundo Zazikulu za M’kalata ya Aroma

3:⁠4. Zonena za anthu zikasemphana ndi zimene Mulungu amanena m’Mawu ake, ife timalola kuti “Mulungu akhale wonena zoona.” Timatelo mwa kukhulupilila uthenga wa m’Baibulo ndi kucita cifunilo ca Mulungu. Tikamagwila mwacangu nchito yolengeza Ufumu ndi kupanga ophunzila, timathandiza ena kuzindikila kuti Mulungu amanena zoona.

w08 6/15 peji 29 pala. 6

Mfundo Zazikulu za M’kalata ya Aroma

3:​24, 25​—⁠Kodi “dipo lolipilidwa ndi Khristu” linaphimba bwanji “macimo amene anacitika kale,” dipolo lisanalipilidwe? Ulosi woyamba wonena za Mesiya wopezeka pa Genesis 3:​15, unakwanilitsidwa mu 33 C.E., pamene Yesu anaphedwa pa mtengo wozunzikilapo. (Agal. 3:​13, 16) Yehova atangonena ulosiwu, kwa iye dipolo linakhala ngati lapelekedwa kale, cifukwa palibe ciliconse cimene cingalepheletse Mulungu kukwanilitsa colinga cake. Conco, pamaziko a nsembe imene Yesu Khristu anali kudzapeleka, Yehova anakhululukila macimo a mbadwa za Adamu zimene zinakhulupilila lonjezo limenelo. Ndiponso anthu omwe anafa Cikhristu cisanayambe, adzaukitsidwa cifukwa ca dipo limeneli.​—⁠Mac. 24:⁠15.

FEBRUARY 11-17

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 4-6

“Mulungu Akuonetsa Cikondi Cake Kwa Ife”

w11 6/15 peji 12 pala. 5

Mulungu Akuonetsa Cikondi Cake Kwa Ife

5 Poyamba Paulo anafotokoza kuti: ‘Ucimo unaloŵa m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa uchimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.’ (Aroma 5:12) Timadziŵa bwino zimenezi cifukwa cakuti Mulungu anauzila anthu kuti alembe mmene moyo wa anthu unayambila. Yehova analenga anthu aŵili oyambilila, omwe ndi Adamu ndi Hava. Mlengi ndi wangwilo ndipo makolo athu oyambililawo analinso angwilo. Mulungu anawapatsa lamulo limodzi lokha ndipo anawauza kuti ngati samvela lamulolo adzafa. (Gen. 2:17) Koma iwo anasankha kucita zinthu zowawonongetsa. Anaphwanya lamulo losavuta kutsatilali ndipo pocita zimenezi anakana zoti Mulungu ndi woyenela kuwapatsa malamulo ndiponso kuwalamulila.​—⁠Deut. 32:​4, 5.

w11 6/15 peji 12 pala. 6

Mulungu Akuonetsa Cikondi Cake Kwa Ife

6 Adamu anayamba kukhala ndi ana atacimwa kale conco anapatsila anawo ucimo ndiponso zotsatila zake. Anawo sanaphwanye lamulo la Mulungu limene Adamu anaphwanya cotelo iwo sanaimbidwe mlandu wofanana ndi iyeyo. Komanso pa nthawiyo anali asanapatsidwe malamulo. (Gen. 2:17) Komabe ana a Adamu anatengela ucimowo. Conco ucimo ndi imfa zinalamulila mpaka nthawi imene Mulungu anapatsa Aisiraeli malamulo. Malamulowo anawathandiza kuzindikila kuti ndi ocimwa. (Ŵelengani Aroma 5:​13, 14.) Zotsatila za ucimo umene tinatengela tingaziyelekeze ndi matenda amene munthu amapatsila mwana wake. N’zoona kuti si ana onse amene amatengela ngakhale ngati makolo awo akudwala matendawo. Koma si mmene zilili ndi ucimo. Mwana aliyense amatengela ndipo amavutika nawo. Nthawi zonse zotsatila zake ndi imfa. Kodi pali njila iliyonse yothetsela vutoli?

w11 6/15 peji 13 mapa. 9-10

Mulungu Akuonetsa Cikondi Cake Kwa Ife

9 Kodi mawu acigiriki amene anawamasulila kuti “achedwe olungama” ndiponso akuti “akuyesedwa olungama” akutanthauza ciani? Munthu wina womasulila Baibulo anati: “Mawu amenewa akufotokoza zinthu ngati zikucitika m’khoti motsatila malamulo. Mawuwa akusonyeza kuti Mulungu wasintha mmene akuonela munthu osati kuti munthuyo wasintha . . . Zili ngati kuti munthu akuimbidwa mlandu wakuti ndi wosalungama ndipo Mulungu ndi woweluza yemwe wagamula kuti munthuyu amasulidwe.”

10 Kodi “Woweluza wa dziko lonse lapansi” angamasule munthu wosalungama pa zifukwa ziti? (Gen. 18:25) Kuti izi zitheke, Mulungu anatumiza Mwana wake wobadwa yekha kudziko lapansi. Anacita zimenezi cifukwa ca cikondi. Yesu anacita cifunilo ca Atate ake popanda kulakwitsa kalikonse, ngakhale kuti anayesedwa, kunyozedwa kwambili ndiponso kuzunzidwa. Iye anakhalabe wokhulupilika mpaka pamene anaphedwa pamtengo wozunzikilapo. (Aheb. 2:10) Yesu anapeleka moyo wake wangwilo monga dipo lomasula kapena kuwombola ana a Adamu ku ucimo ndi imfa.​—⁠Mat. 20:28; Aroma 5:​6-8.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w08 6/15 peji 29 pala. 7

Mfundo Zazikulu za M’kalata ya Aroma

6:​3-5​—⁠Kodi kubatizidwa mu mgwilizano ndi Khristu Yesu komanso kubatizidwa mu imfa yake, kukutanthauza ciani? Yehova akadzoza otsatila a Khristu ndi mzimu woyela, iwo amagwilizana ndi Yesu ndi kukhala ziwalo za mpingo umene ndi thupi la Khristu, ndipo Yesu ndiye Mutu. (1 Akor. 12:​12, 13, 27; Akol. 1:18) Kumeneku ndiko kubatizidwa mu mgwilizano ndi Khristu Yesu. Akhristu odzozedwa ‘amabatizidwanso mu imfa’ ya Khristu m’njila yakuti amakhala ndi moyo wodzimana ndipo amasiya ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Conco imfa yawo imakhala nsembe ngati imfa ya Yesu, ngakhale kuti imfa yawoyo si dipo lowombola anthu. Ubatizo wa mu imfa ya Khristu umenewu umamalizidwa odzozedwawo akamwalila n’kuukitsidwa kukakhala ndi moyo kumwamba.

w14 6/1 peji 31 pala. 1

Kodi Makolo Akale Omwe Anamwalila Adzakhalanso ndi Moyo?

Kodi osalungama akadzaukitsidwa adzaweluzidwa potengela zimene anacita asanamwalile? Ayi. Lemba la Aroma 6:7 limati: “Cifukwa munthu amene wafa wamasuka ku ucimo wake.” Pamene anthu osalungamawa anamwalila, ndiye kuti analipila mtengo wa macimo awo. Conco adzaweluzidwa potengela zimene adzacite akadzaukitsidwa, osati zimene anacita asanamwalile. Kodi iwo adzapindula bwanji ndi zimenezi?

FEBRUARY 18-24

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 7-8

“Kodi Mukuyembekezela Mwacidwi?”

w12 7/15 peji 11 pala. 17

Lolani Yehova Kukutsogolelani ku Ufulu Weni-weni

17 Pofotokoza za ufulu umene Yehova adzapatse atumiki ake padziko, Paulo analemba kuti: “Cilengedwe cikudikila mwacidwi nthawi imene ulemelelo wa ana a Mulungu udzaonekele.” Kenako anati: “Cilengedweco cidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:​19-21) Mawu oti “cilengedwe” akunena za anthu amene ali ndi ciyembekezo cokhala padziko lapansi. Iwo adzapindula pamene ulemelelo wa ana a Mulungu “udzaonekele.” Ulemelelowu udzayamba kuonekela ‘anawa’ ataukitsidwila kumwamba. Udzaonekela akamadzathandiza Khristu kucotsa zoipa zonse padziko ndiponso kupulumutsa “khamu lalikulu” kuti liloŵe m’dziko latsopano.​—⁠Chiv. 7:​9, 14.

w12 3/15 peji 23 pala. 11

Tizisangalala ndi Ciyembekezo Cathu

11 Yehova anapatsa anthu maziko a ciyembekezo pamene analonjeza kuti adzawapulumutsa kwa “njoka yakale,” yomwe ndi Satana Mdyelekezi. Adzacita zimenezi pogwilitsa nchito “mbewu” yolonjezedwa. (Chiv. 12:9; Gen. 3:15) Yesu Khristu ndi mbali yoyamba ya “mbewu” imeneyi. (Agal. 3:16) Imfa ndiponso kuukitsidwa kwa Yesu zimatsimikizila kuti ciyembekezo cimene anthu ali naco, comasulidwa ku ukapolo wa ucimo ndi imfa, cidzathekadi. Kukwanilitsidwa kwa ciyembekezo cimeneci n’kogwilizana ndi “nthawi imene ulemelelo wa ana a Mulungu udzaonekele.” Akhristu odzozedwa ndi mbali yaciŵili ya “mbewu.” Iwo ‘adzaonekela’ pamene adzathandize Khristu powononga dziko la Satana loipali. (Chiv. 2:​26, 27) Izi zidzacititsa kuti nkhosa zina zotuluka m’cisautso cacikulu zipulumutsidwe.​—⁠Chiv. 7:​9, 10, 14.

w12 3/15 peji. 23 pala. 12

Tizisangalala ndi Ciyembekezo Cathu

12 Koma kunena zoona, “cilengedwe” cidzapumuladi mu Ulamulilo wa Zaka 1,000 wa Khristu. Pa nthawi imeneyi, “ana a Mulungu” aulemelelo adzaonekelanso pamene adzagwilanso nchito monga ansembe limodzi ndi Khristu ndipo adzathandiza anthu kupindula ndi nsembe ya dipo ya Yesu. Monga nzika za Ufumu wa Mulungu, anthu adzamasulidwa ku ucimo ndi imfa. Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono, anthu omvela ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda.’ Ngati adzakhalabe okhulupilika kwa Yehova mkati mwa zaka 1,000 mpaka pamapeto pa mayeselo omaliza, mayina awo adzalembedwa mu “mpukutu wa moyo.” Iwo adzalowa mu “ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.” (Chiv. 20:​7, 8, 11, 12) Cimenecitu ndi ciyembekezo cosangalatsa kwambili.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w17.06 peji 3

Kodi Mukumbukila?

Kodi “kuika maganizo pa zinthu za thupi” kusiyana bwanji na “kuika maganizo pa zinthu za mzimu”? (Aroma 8:⁠6)

Munthu woika maganizo ake pa zinthu za thupi amasumika maganizo na mtima wake pa zolakalaka ndi zofuna za thupi lake lopanda ungwilo. Amangokhalila kukamba mokokomeza zinthu za thupi. Koma munthu woika maganizo pa zinthu za mzimu ni amene moyo wake wonse umakhala pa kucita zinthu zokhudzana ndi kulambila Mulungu, ndipo amayesetsa kugwilizanitsa maganizo ake ndi a Mulungu. Mkhristu waconco amalola maganizo ake kutsogoleledwa na mzimu woyela. Kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweletsa imfa, koma kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweletsa moyo ndi mtendele.​—⁠w16.12, mapeji 15-17.

w09 11/15 peji 7 pala. 20

Kodi Mapemphelo Anu Amasonyeza Ciani za Inuyo?

20 Zingacitike nthawi zina kuti sitikudziŵa zoti tinene m’pemphelo laumwini. Paulo ananena kuti: “Pakuti cimene tiyenela kupemphelela monga mmene tiyenela kupemphela sitikucidziŵa, koma mzimu [woyela] umacondelela m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza. Koma iye [Mulungu] amene amasanthula mitima amadziŵa zimene mzimu ukutanthauza.” (Aroma 8:​26, 27) Yehova anaonetsetsa kuti mapemphelo ambili alembedwa m’Malemba. Iye amalandila mapemphelo ouzilidwa amenewa ngati kuti akucokela kwa ife, ndipo amaticitila zimene tinafuna kupemphazo. Mulungu amatidziŵa bwino ndipo amadziŵanso tanthauzo la zimene anauzila mzimu wake kuti ulankhule kudzela mwa anthu amene analemba Baibulo. Yehova amayankha mapembedzelo athu mzimu ‘ukamacondelela’ m’malo mwathu. Koma tikayamba kuwadziŵa bwino Mawu a Mulungu, mfundo zoti tichule m’pemphelo zimabwela msanga m’maganizo mwathu.

FEBRUARY 25–MARCH 3

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 9-11

“Fanizo la Mtengo wa Maolivi”

w11 5/15 peji 23 pala. 13

‘Nzelu za Mulungu N’zozama’ Kwambili’

13 Paulo anayelekeza anthu opanga mbewu ya Abulahamu ndi nthambi za mtengo wa maolivi wophiphilitsila. (Aroma 11:21) Mtengo wa maolivi wobzalidwa umaimila kukwanilitsidwa kwa colinga cimene Mulungu anali naco pamene anacita pangano ndi Abulahamu. Muzu wa mtengowu ndi woyela ndipo umaimila Yehova cifukwa ndi amene amapeleka moyo kwa Aisiraeli auzimu. (Yes. 10:20; Aroma 11:16) Thunthu la mtengowu limaimila Yesu cifukwa cakuti iye ndi mbali yoyamba ya mbewu ya Abulahamu. Nthambi zonse pamodzi zimaimila ‘ciŵelengelo cokwanila’ ca anthu opanga mbali yaciŵili ya mbewu ya Abulahamu.

w11 5/15 peji 24 pala. 15

‘Nzelu za Mulungu N’zozama’ Kwambili’

15 Ndiyeno kodi Yehova anakwanilitsa bwanji colinga cake? Paulo anafotokoza kuti nthambi za mtengo wa maolivi wam’chile zinalumikizidwa kumtengo wa maolivi wobzalidwa kuti ziloŵe m’malo mwa zimene zinadulidwa. (Ŵelengani Aroma 11:​17, 18.) Conco Akhristu odzozedwa ndi mzimu ocokela ku mitundu ina, ngati amene anali mu mpingo wa ku Roma, analumikizidwa mophiphilitsila kumtengo wa maolivi. Izi zinacititsa kuti akhale mbali ya mbewu ya Abulahamu. Poyamba iwo anali ngati nthambi za mtengo wa maolivi wam’chile ndipo analibe mwayi uliwonse wokhala m’pangano lapadelali. Koma Yehova anawapatsa mwayi wokhala Ayuda auzimu.​—⁠Aroma 2:​28, 29.

w11 5/15 peji 25 pala. 19

‘Nzelu za Mulungu N’zozama’ Kwambili’

19 Colinga ca Yehova cokhudza “Isiraeli wa Mulungu” cikukwanilitsidwa m’njila yocititsa cidwi kwambili. (Agal. 6:16) Malinga ndi zimene Paulo ananena, “Aisiraeli onse adzapulumuka.” (Aroma 11:26) Pa nthawi imene Yehova wasankha, “Aisiraeli onse,” kapena kuti ciŵelengelo cokwanila ca Aisiraeli auzimu, adzatumikila monga mafumu ndi ansembe kumwamba. Palibe cimene cingalepheletse colinga ca Yehova.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w13 6/15 peji 25 pala. 5

Lolani Kuti Yehova Azikuumbani Ndi Malangizo Ake

5 Nanga cingacitike n’ciani ngati anthu akana kuumbidwa ndi Mulungu? Taganizilani zimene woumba amacita akaona kuti cinthu cimene akuumba sicikuumbika bwino. Iye angasankhe kuumba cinthu cina kapena akhoza kungotaya dongolo. Nthawi zambili kuti dongo lifike powonongeka, vuto limakhala ndi woumbayo. Koma si mmene zilili ndi Mulungu. (Deut. 32:⁠4) Ngati munthu wina akukanika kuumbidwa ndi Yehova, nthawi zonse vuto limakhala ndi munthuyo. Yehova akamaumba anthu amasintha mogwilizana ndi zimene anthuwo akucita. Anthu amene amalola kuumbidwa, iye amawaumba kuti akhale anthu abwino. Mwacitsanzo, Akhristu odzozedwa ndi “ziwiya zacifundo” omwe aumbidwa kukhala ‘ziwiya zolemekezeka.’ Koma anthu amene amakana kuti Mulungu awaumbe amakhala “ziwiya za mkwiyo zoyenela kuwonongedwa.”​—⁠Aroma 9:​19-23.

it-1 peji 1260 pala. 2

Cangu

Cangu Colakwika. Munthu angakhale wacangu kwambili, kapena kuti wodzipeleka pocita zinazake, koma zimene akucitazo n’kukhala zolakwika komanso zosakondweletsa Mulungu. Umu ni mmene zinalili kwa Ayuda ambili a m’zaka 100 zoyambilila. Iwo anaganiza kuti adzakhala acilungamo kupitila m’nchito zimene anali kugwila pansi pa Cilamulo ca Mose. Koma Paulo anaonetsa kuti cangu cawo cinali colakwika cifukwa analibe cidziŵitso colongosoka. Iwo anafunika kudziŵa vuto lawo na kubwelela kwa Mulungu kupitila mwa Khristu, kuti alandile cilungamo ndi ufulu womasuka ku mlandu wa Cilamulo. (Aroma 10:​1-10) Saulo wa ku Tariso anali m’modzi wa anthu otelo. Anali wacangu copambanitsa m’cipembedzo ca Ayuda cakuti anafika mpaka pa ‘kuzunza kwambili mpingo wa Mulungu ndi kupitilizabe kuuwononga.’ Iye anali kutsatila Cilamulo mosamala kwambili, ndipo ‘anakhala wopanda cifukwa comunenezela.’ (Agal. 1:​13, 14; Afil. 3:⁠6) Cangu ca Saulo pa Ciyuda cinali colakwika. Koma iye anali kucita zinthu moona mtima. Pa cifukwa cimeneci, Yehova anamuonetsa kukoma mtima kwake kosatha kupitila mwa Khristu, pomusintha kukhala Mkhristu woona.​—⁠1 Tim. 1:​12, 13.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani