NYIMBO 36
Titeteze Mitima Yathu
Yopulinta
(Miyambo 4:23)
1. Titeteze mtima wathu,
Tipewe ucimo.
Yehova adziŵa zonse
Za mu mtima mwathu.
Nthawi zina mtima wathu
Ungatinamize.
Conco tiganize bwino,
Timvele Yehova.
2. Tikonzekeletse mtima,
Tifune Yehova.
Tim’tamande, tim’yamike,
Amatisamala.
Malangizo a Yehova,
Tidzawatsatila.
Tifuna kum’kondweletsa,
Tsiku lililonse.
3. Titeteze mtima wathu
Ku zinthu zoipa.
Mau a Yehova M’lungu
Adzatithandiza.
Yehova adzatikonda
Ngati tiyesetsa.
Yehova ni bwenzi lathu.
Ise tim’lambile.
(Onaninso Sal. 34:1; Afil. 4:8; 1 Pet. 3:4.)