NYIMBO 128
Pilila Mpaka Mapeto
Yopulinta
1. Zimene mau a M’lungu
Amatilonjeza.
Ise zimatithandiza
Kupilila mavuto.
Ukhale wokhazikika
Pa cikhulupililo.
Usaiŵale za Tsiku
La Yehova Mulungu.
2. Usayope, usagonje,
Zivute zitani.
Usaleke kumukonda
Yehova ‘tate wathu.
Olo uyesedwe bwanji
Iwe usakaike.
Nthawi zonse M’lungu wako
Ali pafupi nawe.
3. Opilila mosaleka
Adzapulumuka.
Olo agone mu imfa
Yehova ‘maŵakonda.
Conco iwe upilile
Mpaka cabe mapeto.
M’lungu sadzakuiŵala.
Udzasangalaladi.
(Onaninso Aheb. 6:19; Yak. 1:4; 2 Pet. 3:12; Chiv. 2:4.)