LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 29 tsa. 74-tsa. 75 pala. 2
  • Yehova Asankha Yoswa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Asankha Yoswa
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Yoswa Akhala Mtsogoleli
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Aoloka Mtsinje Wa Yorodano
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Azondi 12
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 29 tsa. 74-tsa. 75 pala. 2
Ansembe anyamula likasa la cipangano powoloka Mtsinje wa Yorodano

PHUNZILO 29

Yehova Asankha Yoswa

Yoswa aŵelenga mu Cilamulo

Mose anatsogolela Aisiraeli kwa zaka zambili. Koma apa lomba, anali pafupi kumwalila. Conco Yehova anamuuza kuti: ‘Sindiwe udzaloŵetsa Aisiraeli m’Dziko Lolonjezedwa. Koma nidzakuonetsa dzikolo.’ Ndiyeno Mose anapempha Yehova kuti asankhe munthu wina kuti atsogolele anthu ake. Yehova anamuyankha kuti: ‘Pita kwa Yoswa, ndipo ukamuuze kuti ndam’sankha kukhala mtsogoleli.’

MMose anauza Aisiraeli kuti iye adzamwalila posacedwa, na kuti Yehova wasankha Yoswa kuti awatsogolele ku Dziko Lolonjezedwa. Ndiyeno Mose anauza Yoswa kuti: ‘Usacite mantha. Yehova adzakuthandiza.’ Pasanapite nthawi yaitali, Mose anakwela pamwamba m’Phili la Nebo, ndipo Yehova anamuonetsa dziko limene analonjeza Abulahamu, Isaki, na Yakobo. Kenako Mose anamwalila, ali na zaka 120.

Mose aika Yoswa kukhala mtsogoleli pamaso pa wansembe ndi amuna ena

Ndiyeno Yehova anauza Yoswa kuti: ‘Woloka Mtsinje wa Yorodano, uloŵe m’dziko la Kanani. N’dzakuthandiza monga mmene n’nathandizila Mose. Ndipo uonetsetse kuti ukuŵelenga Cilamulo canga tsiku lililonse. Usacite mantha, limba mtima. Pita ukacite zimene ndakuuza.’

Yoswa anatuma azondi aŵili ku mzinda wa Yeriko. M’nkhani yokonkhapo, tidzaphunzila zimene zinacitika mu mzinda umenewu. Atabwelako azondiwo, anati inali nthawi yabwino yokaloŵa m’dziko la Kanani cifukwa anthu anali na mantha. M’maŵa mwake, Yoswa anauza Aisiraeli kuti apasule msasa. Ndiyeno, anauza ansembe onyamula likasa la cipangano kukhala patsogolo pokawoloka Mtsinje wa Yorodano. Mtsinjewo unali wosefukila. Koma pamene ansembe anaponda m’madzi, mtsinjewo unaleka kuyenda, ndipo madzi anapita. Ansembe anapita kukaima pakati pa mtsinje, ndipo mtundu wonse wa Isiraeli unawolokela ku tsidya linalo. Uganiza bwanji, kodi cozizwitsa ici sicinawakumbutse zimene Yehova anacita pa Nyanja Yofiila?

Lomba, pambuyo pa zaka zambili, Aisiraeli analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Anayamba kumanga manyumba na mizinda. Anayamba kulima mphesa, zipatso, na mbewu zina. Linalidi dziko loyenda mkaka na uci.

“Yehova azidzakutsogolelani nthawi zonse ndipo adzakukhutilitsani ngakhale m’dziko louma.”—Yesaya 58:11

Mafunso: N’ndani anatsogolela Aisiraeli Mose atamwalila? Nanga n’ciani cinacitika pa Mtsinje wa Yorodano?

Numeri 27:12-23; Deuteronomo 31:1-8; 34:1-12; Yoswa 1:1–3:17

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani