NYIMBO 80
‘Talaŵani, Muone Kuti Yehova ni Wabwino’
Yopulinta
(Salimo 34:8)
1. Tikonda kutumikila
Yehova Atate wathu.
Tidzipeleka na mtima wonse
Kuti’fe tilalikile.
(KOLASI)
Mau a M’lungu aitana:
‘Talaŵani muone.
Kuti Yehova ni wabwino.’
Mudzadalitsidwadi.
2. Mtumiki wanthawi zonse
Amapeza madalitso.
Pa zofunika za moyo wake
Amadalila Yehova.
(KOLASI)
Mau a M’lungu aitana:
‘Talaŵani muone.
Kuti Yehova ni wabwino.’
Mudzadalitsidwadi.
(Onaninso Maliko 14:8; Luka 21:2; 1 Tim. 1:12; 6:6.)