NYIMBO 90
Tilimbikitsane Wina na Mnzake
Yopulinta
(Aheberi 10:24, 25)
1. Pamene tilimbikitsana
Kutumikila Yehova.
Cikondi cathu cimakula;
Timapezadi cimwemwe.
Cikondi timaonetsana,
Cimatilimbikitsadi.
Mpingo ni pothaŵila pathu,
Ni malo a citetezo.
2. Mwa mau athu acikondi
Timatonthozadi ena.
Ndipo timaŵalimbikitsa
Kuti iwo asafo’ke.
Kumatipatsadi cimwemwe
Kuseŵenzela pamodzi.
Conco tizilimbikitsana
Ndipo tizithandizana.
3. Tsiku la Atate Yehova,
Tidziŵa layandikadi.
Tifunika tizisonkhana
Kuti tikapulumuke.
Tiyeni tizithandizana
Kusunga umphumphu wathu.
Monga banja logwilizana
Tidzalimbikitsanadi.
(Onaninso Luka 22:32; Mac. 14: 21, 22; Agal. 6:2; 1 Ates. 5:14.)