LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g21 na. 1 masa. 8-9
  • Zinsinsi Zotithandiza Kukhala Okhutila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zinsinsi Zotithandiza Kukhala Okhutila
  • Galamuka!—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Muzigwila Nchito Molimbikila
  • Khalani Woona Mtima
  • Muziona Ndalama Moyenela
  • Sankhani Maphunzilo Abwino Kwambili
  • Kodi Ndalama N’zimene Zimabweletsa Mavuto Onse?
    Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
  • Mmene Mungagwilitsile Nchito Ndalama
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Kodi Baibo Imakamba Ciyani pa Zanchito Komanso Ndalama?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Muzikondwela Nayo Nchito Yanu
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
Onaninso Zina
Galamuka!—2021
g21 na. 1 masa. 8-9
Mayi na mwana wake wamwamuna ali ku mashopu okhala na anthu ambili ku India, ndipo ni okhutila na zimene ali nazo. Kumeneko kuli anthu okonda zinthu zapamwamba.

Zinsinsi Zotithandiza Kukhala Okhutila

Tonse, kaya ndife okwatila kapena ayi, acicepele kapena acikulile, timafuna kukhala acimwemwe komanso okhutila. N’zimenenso Mlengi wathu amafuna. N’cifukwa cake iye watipatsa malangizo othandiza kwambili.

Muzigwila Nchito Molimbikila

“Agwile nchito molimbikila. Agwile ndi manja ake nchito yabwino, kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.”—AEFESO 4:28.

Mlengi wathu amafuna tiziona kuti kugwila nchito ni cinthu cabwino. Cifukwa ciani? Munthu amene amagwila nchito molimbika amakhala wokondwela, cifukwa amakwanitsa kudzisamalila komanso kusamalila banja lake. Angakwanitsenso ngakhale kuthandiza wina amene ni wosoŵa. Nawonso abwana ake amam’konda. Conco ngati munthu amaseŵenza mwakhama si kwenikweni kucotsedwa nchito. Mpake kuti Malemba amafotokoza zotulukapo zabwino za kugwila nchito mwakhama kuti ni “mphatso yocokela kwa Mulungu.”—Mlaliki 3:13.

Khalani Woona Mtima

“Tikukhulupilila kuti tili ndi cikumbumtima coona, popeza tikufuna kucita zinthu zonse moona mtima.”—AHEBERI 13:18.

Tikakhala oona mtima, timadzisungila ulemu. Timakhala na mtendele wa maganizo, ndiponso timagona tulo twabwino. Kuwonjezela apo, anthu ena amatikhulupilila na kutilemekeza. Koma anthu osaona mtima amadzimana zinthu zabwino zimenezi. Cina, cikumbumtima cawo cingamawavutitse, ndipo angamakhale mwamantha poopa kuti tsiku lina adzagwidwa cifukwa ca kusakhulupilika kwawo.

Muziona Ndalama Moyenela

“Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.”—AHEBERI 13:5.

Timafunika ndalama zogulila cakudya na zinthu zina zofunikila. Komabe, “kukonda ndalama” n’koopsa. Kungapangitse munthu kuthela nthawi yoculuka na mphamvu zake posakila ndalama. Zimenezi zingabweletse mavuto m’cikwati cake, zingamulande nthawi yoceza na ana ake, ndipo zingawononge ngakhale thanzi lake. (1 Timoteyo 6:9, 10) Kuwonjezela apo, munthu amene amakonda ndalama angakhale pa mayeselo ocita zinthu mosakhulupilika. Munthu wina wanzelu analemba kuti: “Munthu wocita zinthu mokhulupilika adzapeza madalitso ambili, koma woyesetsa kuti apeze cuma mofulumila, sadzapitiliza kukhala wosalakwa.”—Miyambo 28:20.

Sankhani Maphunzilo Abwino Kwambili

“Usunge nzelu zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.”—MIYAMBO 3:21.

Maphunzilo abwino angatithandize kukhala anthu odalilika komanso kukhala makolo abwino. Koma maphunzilo abwino akuthupi paokha sangatipatse citetezo cokhalitsa kapena cimwemwe. Kuti zinthu zizitiyendela bwino pa zilizonse zimene timacita, tiyenela kulandila maphunzilo ocokela kwa Mulungu. Pokamba za munthu amene amamvela Mulungu, Malemba amati: “Zocita zake zonse zidzamuyendela bwino.”—Salimo 1:1-3.

Ndine Wacimwemwe Komanso Wokhutila

“M’dela limene nimakhala, anthu ambili amacita khama kuti apeze maphunzilo apamwamba, cuma, komanso kuti akhale ochuka. Olo n’telo, iwo sapeza cimwemwe cokhalitsa ngakhale pambuyo pokwanilitsa zolinga zawo. Koma Baibo inanithandiza kudziŵa zinthu zofunika kwambili pa umoyo. N’naphunzila kuti ndalama zingatiteteze m’njila zina. Koma sizingagule cimwemwe kapena cikondi ceniceni. Tsopano ndine wacimwemwe na wokhutila cifukwa Baibo imanithandiza kupanga zisankho zanzelu pankhani ya ndalama na nchito.”—Kishore.

Kishore.

Phunzilani zambili:

Kuti mupeze malangizo owonjezeleka ocokela kwa Mlengi pa nkhani za nchito, ndalama, na maphunzilo, pitani pa jw.org ku Chichewa na kuona pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MTENDERE KOMANSO MOYO WOSANGALALA.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani