Salimo
113 Tamandani Ya!*
Inu atumiki a Yehova, mutamandeni,
Tamandani dzina la Yehova.
2 Dzina la Yehova litamandike
Kuyambira panopa mpaka kalekale.+
3 Kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera,
Dzina la Yehova litamandidwe.+
6 Iye amatsika mʼmunsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi.+
7 Amadzutsa munthu wonyozeka kumuchotsa mʼfumbi.
Amanyamula munthu wosauka kumuchotsa pamulu wa phulusa*+
8 Kuti amukhazike pamodzi ndi anthu olemekezeka,
Pamodzi ndi anthu olemekezeka pakati pa anthu a Mulungu.
Tamandani Ya!*