Salimo
BUKU LACHITATU
(Masalimo 73-89)
Nyimbo ya Asafu.+
73 Mulungu ndi wabwinodi kwa Isiraeli, kwa anthu oyera mtima.+
2 Koma ine mapazi anga anangotsala pangʼono kusochera,
Mapazi anga anangotsala pangʼono kuterereka.+
5 Iwo savutika ngati mmene anthu ena amavutikira,+
Ndipo sakumana ndi mavuto mofanana ndi anthu ena.+
6 Choncho kudzikuza kuli ngati mkanda mʼkhosi mwawo,+
Ndipo avala chiwawa ngati malaya.
7 Maso awo akwiririka chifukwa cha kunenepa kwa nkhope yawo.*
Ali ndi zinthu zambiri kuposa zimene ankalakalaka mumtima mwawo.
8 Iwo amanyodola komanso kulankhula zinthu zoipa.+
Amaopseza anthu monyada kuti awapondereza.+
9 Amalankhula ngati kuti ali kumwamba,
Ndipo malilime awo akuyendayenda padziko lapansi mwamatama.
10 Choncho anthu a Mulungu amawatsatira,
Ndipo amamwa madzi awo omwe ndi ambiri.
11 Iwo amanena kuti: “Mulungu angadziwe bwanji?+
Kodi Wamʼmwambamwamba amadziwa chilichonse?”
12 Ndithudi, izi nʼzimene oipa amachita, amakhala mosatekeseka nthawi zonse.+
Iwo amawonjezera chuma chawo.+
13 Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe,
Ndipo ndasamba mʼmanja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wosalakwa.+
15 Koma ndikananena zinthu zimenezi,
Ndikanachitira chinyengo anthu anu.*
16 Nditayesa kuti ndimvetse zimenezi,
Zinali zopweteka kwa ine
17 Mpaka pamene ndinalowa mʼmalo opatulika aulemerero a Mulungu,
Ndipo ndinazindikira tsogolo lawo.
18 Ndithudi, mwawaika pamalo oterera.+
Mwawagwetsa kuti awonongeke.+
19 Iwo awonongedwa mwadzidzidzi.+
Afika pamapeto awo modzidzimutsa ndipo atha momvetsa chisoni!
20 Inu Yehova, mofanana ndi maloto amene amaiwalika munthu akadzuka,
Inunso mukadzuka mudzawakana.*
22 Ndinali wopanda nzeru ndipo sindinkamvetsa zinthu.
Ndinali ngati nyama yosaganiza pamaso panu.
23 Koma tsopano ine ndili ndi inu nthawi zonse.
Mwandigwira dzanja langa lamanja.+
25 Winanso ndi ndani kumwambako amene angandithandize?
Ndipo chifukwa chakuti inu muli ndi ine, palibenso chimene ndimalakalaka padziko lapansi.+
26 Thupi langa ndi mtima wanga zingalefuke,
Koma Mulungu ndi thanthwe la mtima wanga ndiponso cholowa changa mpaka kalekale.+
27 Ndithudi, anthu amene ali kutali ndi inu adzatheratu.
Mudzawononga* aliyense amene akukusiyani pochita chigololo.*+
28 Koma kwa ine, kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.+
Ndapanga Yehova Ambuye Wamkulu Koposa kukhala malo anga othawirako,
Kuti ndilengeze za ntchito zanu zonse.+